Chichewa

Boma likweza aphunzitsi 20 210

Listen to this article

Bungwe la aphunzitsi m’dziko muno la Teachers Union of Malawi (TUM) lati ndilokondwa ndi kukwezedwa kwa aphunzitsi 20 210 a m’sukulu za pulayimale ndi sekondale.

Anthu ena akuti boma la DPP lachita izi pofuna kukopa aphunzitsi kuti adzachivotere pa zisankho zapatatu zomwe zidzachitike m’dziko muno pa May 21.

Saidi: Sizikugwirizana ndi kampeni

Boma lidakweza aphunzitsi kotsiriza m’chaka cha 2013 pamene dziko lino limayandikira zisankho za m’chaka cha 2014.

TUM yakhala ikupempha boma kuti likweze aphunzitsi, koma pempho lawo silimaphula kanthu.

Koma mwezi wa January chaka chino boma lidalengeza kuti likweza aphunzitsi, zomwe zidautsa mafunso mwa anthu ambiri omwe akuganiza kuti boma likungofuna kupeza mavoti kuchokera kwa aphunzitsiwo.

Mkulu wa bungwe lopititsa patsogolo ufulu wa maphunziro m’dziko muno la Civil Society Education Coalition (Csec), Benedicto Kondowe, adauza nyuzipepala ya The Nation  kuti aphunzitsi ambiri atenga zaka zoposa 10 osakwezedwa.

Kondowe adati mwina n’kutheka kuti boma lidakonza kale ndondomeko yoti lidzakweze aphunzitsi nthawi ya kampeni ikadzafika.

Mlembi wa TUM, Charles Kumchedwa, agwirizana ndi Kondowe kuti aphunzitsi ambiri atenga nthawi yaitali osakwezedwa moti ndi wokondwa kuti boma lamva kulira kwawo.

“Ife za kampeni tilibe nazo ntchito, nkhani ndi yoti aphunzitsi akwezedwa,” adatero Kumchenga.

Mlembiyu adapempha boma kuti lipereke msanga makalata kwa aphunzitsi onse okwezedwa, komanso kuwakonzera msanga malipiro awo atsopano.

Kumchenga adati TUM idapempha boma kuti likweze aphunzitsi 40 000-a ku pulayimale 25 000 ndi 15 000 a ku sekondale.

Mmbuyomu mkuluyu adauza Tamvani kuti aphunzitsi onse alipo 80 000.

Malingana ndi kalata yomwe boma latulutsa Lachitatu pa April 3 ndipo yasainidwa ndi mlembi wa mkulu wa mu unduna wa za maphunziro, Justin Saidi mogwirizana ndi wa mu unduna wa maboma aang’onoang’ono, Charles Kalemba, mwa aphunzitsi 20 210 omwe akwezedwa 15 491 ndi a ku pulayimale pamene 4 719 ndi a ku sekondale.

Saidi adati kukwezedwa kwa aphunzitsiwo sikukugwirizana ndi kampeni, koma kuti nthawi yawo yangokwana.

Iye adati aphunzitsi onse okwezedwa  alandira ndalama zawo mwachangu kaamba koti zidalowa kale mu ndondomeko ya za chuma ya chaka chino.

Mayeso okwezera aphunzitsiwo adayamba mwezi wa January ndipo atha mwezi watha.

Related Articles

Back to top button