Chichewa

‘Boma lisavomereze kuchotsa pathupi’

 

Potsatira zomwe ndinalemba sabata yatha, mmodzi wa awerengi watumiza maganizo ake motere:

 

Rabecca,

Ndine mmodzi mwa amene ndimatsatira zimene umalemba patsamba ili ndipo sindinagwirizane ndi maganizo omwe udalemba sabata yatha kuti ndi bwino malamulo a dziko lino alole amayi omwe akufuna kuti azitha kuchotsa pakati m’zipatala.

Ndikudziwa pali mavuto omwe akudza kaamba koti anthu akuchotsa pakati pogwiritsa ntchito njira zoopsa zomwe zikumavulaza kapena kupha amayi ndi atsikana, komabe yankho la mavutowa si kuvomereza kuti anthu azingotaya pakati mwachisawawa.

Ine ndimakhulupirira kuti moyo ndi mphatso ya mtengo wapatali yomwe Namalenga amapereka kwa munthu. Malembo amanenetsa kuti tisanabadwe kapena kuti munthu asanapangidwe n’komwe m’mimba mwa mayi wake, Mulungu amakhala atamudziwa kale.

Kwa ine, izi zikusonyeza kuti pathupi paliponse pamapangidwa ndi Mulungu amene amapereka moyo, posaona kuti wotenga pathupiyo akadali pasukulu, wagwiririridwa kaya sadalowe m’banja.

Ndiye ngati Mulungu walola kuti woterewa akhale woyembekezera ndiye kuti amakhala ndi cholinga ndi moyo wa mwana akuyembekezeredwayo, choncho n’cholakwika kuti mayiyo aloledwe kuti azichotsa moyowo.

Ngati chamukomera Mulungu kuti pakhale moyo, Mulunguyo amadziwa kuti mwana wobadwayo asamalidwa bwanji. Timaona anthu amisala akubereka ana n’kumakula m’matauni ndi m’mizindamu. Ngati munthu wamisala akutha kulera mwana, kuli bwanji anthu alungalunga?

Mwina simunaonepo, koma ine ndikudziwa za ana ena omwe adabadwa makolo awo ali pasukulu kapena sadalowe m’banja, ndipo ndikamba pano anawa ndi anthu ofunikira omwe amapindulira dziko liko komanso kuthandiza makolo awo.

Izi zomati anthu azichotsa mimbazi zimangoyang’ana mavuto alero osaunikira kutsogolo komanso cholinga cha Mulungu pokulola kuti ukhale ndi pathupi.

Ndikudziwa kuti kutenga pathupi uli pasukulu kapena usanapeze banja zimaoneka ngati zolakwika, koma izi zisapangitse kuchotsa pathupi kukhala ngati ndi chithu cholungama.

Ndine mayi Banda,

Blantyre.

Related Articles

Back to top button