Chichewa

Bwanji nkhuku yoweta sagula pamsika?

Listen to this article

Achewa ali ndi njira zosiyanasiyana zoperekera malango pakati pawo. Njira zina ndi monga nthano, magule, ndakatulo, chinamwali ndi miyambi ndi zining’a. Lero nkhani yathu yagona pa miyambi ndipo tifukula mwambi wakuti ‘nkhuku yoweta sagula pamsika’. STEVEN PEMABMOYO adacheza ndi mfumu yaikulu Njewa ya ku Lilongwe, yomwe ikutambasula za mwambiwu.

Choyamba, mfumu, tafotokozani za momwe nkhani ya chikhalidwe cha makolo ilili kuno.

Kwathu kuno ndi dera limodzi lomwe anthu sataya chikhalidwe cha makolo ndipo kuti mukhale pakati pathu kwa masiku angapo mukhoza kuona kusintha poyerekeza ndi zomwe mudazolowera kuona. Anthu a kuno adamva mwambo ndipo adausunga.

Njewa kufotokoza za tanthauzo la mwambiwo
Njewa kufotokoza za tanthauzo la mwambiwo

Tsono mukati adamva mwambo mukufuna kunena kuti adaumva bwanji?

Pakati pa Achewa, mwambo ndi chuma chosiyirana. Makolo kalero adasiyira ana awo omwe adasiyiranso ana awo chonchoo mpakana lero timangosiyirana kuti mpakana kalekale mtundu wathu usadzasokonekere ayi.

 

Ndikufuna kudziwa kusiyiranako mumachita kupatsana pamanja?

Ayi, mwambo si chithu choti mungachione kapena kuchigwira. Imakwana nthawi yoti makolo amadziwa kuti mwana uyu akufunika kudziwa zakuti ndiye amakonza njira yomupatsira mwambo womwe ukufunikawo. Pali njira zingapo monga kutengera mwana kutsimba, kudambwe, kumuitanira anamkungwi kapena kudzera m’miyambi yomwe amatolamo tanthauzo.

 

Eya pamenepo, pali mwambi uja amati nkhuku yoweta sagula pamsika. Mwambi umenewu uli ndi tanthauzo ndithu?

Kwabasi, mwambi umene uja uli ndi tanthauzo lozama kwambiri ndipo mwachita bwino kusankha mwambi umenewu chifukwa umakhudzana ndi moyo wa munthu, makamaka akakula, kuti akukalowa m’banja n’kukayamba moyo wina.

 

Ndikufuna mumasule bwinobwino kuti nkhuku ikubweramo bwanji.

Chabwino, ndiyambe ndi kumasulira motere: munthu ukafuna nkhuku yoti uwete, supita pamsika chifukwa akhoza kukugulitsa yodzimwera mazira kapena yoti idatopa kale kuikira ndiye kuti palibe chomwe wachitapo. Pokagula nkhuku yoweta umafika pakhomo pomwe pali khola ndipo umafunsa

umboni woti nkhukuyo ikadaikira kapena isadayambe nkomwe ndipo kuti mtundu wake umaikira motani. Apa zimatanthauza kuti munthu akafuna banja sangangopita pamsewu nkutengana ndi mkazi kapena mwamuna osadziwa mbiri yake, komwe amachokera ndi mtima wake.

 

Koma amayenera kutani?

Munthu wanzeru amayenera kupita kwa makolo kapena abale a munthu yemwe wamukonda kukaonako ndi kuphunzira khalidwe lawo. Akhozanso kufufuza kudzera kwa anthu adera omwe amakhala kufupi ndi munthuyo, akakhutira akhoza kuyambapo dongosolo. Izi ndi zomwe makolo amatanthauza m’mwambiwu.

 

Paliso pena pomwe mwambiwu ungagwire ntchito?

Kwinako zikhoza kutengera kuti pali nkhani yanji koma bola tanthauzo lake likhale loti pakufunika kusamala, makamaka kuchita kafukufuku osangophwanyirira pochita zinthu. Koma gwero lenileni makolowo poyambitsa mwambiwu adayambitsira nkhani ya maukwati.

 

Koma mukuona kuti zimathandizadi kuti achinyamata amatsatira?

Umboni umenewo ndiye ndili nawo wambiri chifukwa maukwati akamachitika kwathu kuno mafumu amadziwitsidwa ndipo timaona kuti asankhana bwanji mpaka makolo amaitanidwa n’kufunsidwa ngatidi akhutira ndipo ambiri amavomera kuti akhutira kusonyeza kuti anawo ali ndi mwambo, adamvera makolo sadasankhe molakwika.n

Related Articles

Back to top button