Chaka chino kuli zokolola mpweche

Unduna wa zamalimidwe, mthirira ndi chitukuko cha madzi walengeza kuti chaka chino alimi akolola matani 3.3 miliyoni a chimanga kuyerekeza ndimatani 2.6 miliyoni omwe adakololedwa chaka chatha.

Izi zadziwika undunawu utachita kauniuni woyamba wa chiyembekezo cha kakololedwe kaulimi wa 2018/19 ndipo zotsatirazi zikutanthauza kuti chaka chino alimi a chimanga aonjezera makilogalamu 25 pa makilogalamu 100 aliwonse womwe tidapata chaka chatha.

Chaka chilichonse undunawo umapanga kauniuni katatu wa chiyembekezo pa zokolola kuti uwone ngati n’koyenera kuti alimi ndi boma agulitseko zina kapena ayi.

“Kauniuni ameneyu ndi wofunika chifukwa ndi amene amatithandiza kuona ngati m’dziko mukhale chakudya chokwanira kapena ayi. Zimatithandizanso popanga mitengo ya mbewu ndi kuunikira alimi pa nkhani yogulitsa mbeu zawo,” idatero nduna ya zamalimidwe Joseph Mwanamvekha.

Mkulu wa bungwe la Civil Society Agriculture Network (Cisanet) Pamela Kuwali wati nkhaniyi ndi yabwino bola zinthu zisatembenuke mukauniuni awiri otsatira.

Iye waunikira kuti boma ndi mabungwe achilimike potsogolera alimi momwe angasungire mbewu zawo ndi kuzipezera msika wabwino kuti adzapange nazo phindu.

“Chomwe chimachitika n’choti poti zachuluka, mavenda amatsitsa mitengo yogulira mbewu ndiye poti alimi amakhala ndi njala ya ndalama, amangolola mtengo uliwonse osadziwa kuti akubetsa,” watero Kuwali.

Mbiri ya zaka za mmbuyo imasonyeza kuti zotsatira za akauniuni atatuwa zimanka zitsika chifukwa cha zochitika m’dzinja monga kusintha kwa kagwedwe ka mvula, tizirombo toononga mbewu ndi matenda ena adzidzidzi.

Senior Chief Lukwa wa ku Kasungu watsimikiza kuti mmera m’minda ukuoneka bwino ndipo ukupereka chiyembekezo chokolola zochuluka ndipo wati mafumu alandira mabungwe onse omwe aziwapeza ncholinga chophunzitsa alimi kasamalidwe ka zokolola.

Ngakhale ambiri akubwekera kuti mvula ikugwa bwino chaka  chino, Mwanamveka wati kuchuluka kwa zokolola n’chifukwa chapologalamu ya sabuside wafetereza ndi mbeu ya makono.

Iye adati boma lidapanga dala kuwonjezera chiwerengero cha anthu olandira makuponi  afetereza ndi mbeu kuchoka pa 900, 000 mu 2018 kufika pa 1  miliyoni chaka chino kuti alimi ambiri apindule.

Chiyambire pologalamu ya sabuside mchaka cha  2005, boma lagwiritsa ntchito ndalama zokwana K398.6 biliyoni  mu pulogalamuyi koma zokolola zakhala zikulowa pansi mzaka zisanu zapitazo. n

Share This Post

Powered by