Nkhani

Chakwera chenjera—APM

Listen to this article

Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika Lachinayi adachenjeza mtsogoleri wa chipani cha MCP Lazarus Chakwera ponena kuti akukolezera zipolowe za ndale.

Koma Chakwera, polankhula ndi mtolankhani wathu Mutharika atangotha kulankhulako, adati Mutharika ayenera kutulutsa umboni pa zoti akudzetsa mpungwepungwe.

Polankhula ku mtundu wa Amalawi potsatira mpungwepungwe umene wabuka pamene otsatira MCP akhala akuchita zionetsero m’mizinda ya Lilongwe ndi Blantyre komanso maboma Kasungu, Dowa ndi Nkhotakota, Mutharika adati Chakwera achenjere chifukwa kulekerera otsatira MCP kuchita zionetsero kukhonza kuchititsa kuti mwazi ukhetsedwe.

“Zomwe ndinene pano zikhoza kumanga kapena kuphwasula mtundu,” Mutharika adayamba motero. “Ndamvetsedwa kuti Chakwera sakufuna kutsatira za chisankho komanso mfundo za demokalase pobweretsa chisawawa. Akufuna Amalawi atenge boma kupyolera muziwawa. Izi sizitheka.”

Mawu a Mutharika adadza tsiku limene apolisi adaponya utsi wokhetsa misonzi ku maofesi a MCP pomwe Chakwera amakambirana ndi Kazembe wa dziko la America Virginia Palmer amene akumaliza ntchito yake m’dziko lino ndipo wakhala akukumana ndi atsogoleri osiyanasiyana. Izi zidachitikanso pomwe apolisi adamanga otsatira MCP 19, kuphatikizapo phungu wachipanicho mumzinda wa Lilongwe Alfred Jiya.

Mutharika adadzudzula Chakwera ponena kuti akuchita izi pomwe adakatulanso nkhani yotsutsana ndi chisankho kubwalo la milandu. Padakalipano, khoti lapadera lakhazikitsidwa pomwe oweruza milandu asanu akuyembekezeka kugamula ngati zotsatira za chisankho cha pa 21 May zingavomerezedwe kapena ayi.

M’mawu ake, Chakwera adati ayankhapo pa nkhaniyi bwinobwino, koma pakufunika umboni kuti akusokoneza ndiye.

“Abwere ndi umboni. Sindinena zambiri pano mpaka nditakonzeka,” adatero iye.

Chisokonezo chidayamba pomwe bungwe la MEC lidalengeza kuti Mutharika ndiye adapambana chisankhocho, motsatana ndi Chakwera kenako mtsogoleri wa UTM Party Saulos Chilima.

M’sabatayi, otsatira MCP adachita zionetsero makamaka ku Lilongwe komwe mwa zina adathamangitsa ogwira ntchito m’boma kulikulu la boma ku Capital Hill mumzindawo. Iwo adachita izi ngakhale bwalo la milandu lidaluzanitsa milandu ya MCP ndi UTM Party ponena kuti ndi yofanana.

Aneneri a zipani ziwirizo, Maurice Munthali ndi Joseph Chidanti-Malunga adati ndi wokonzeka kuyendetsa limodzi milanduyo.

Katswiri pa za malamulo Edge Kanyongolo adagwirizana ndi zipani ziwirizo pokamang’ala kukhoti chifukwa malamulo amalola zipani kutero ngati sakukhutira ndi momwe chisankho chayendera. Iye adatinso otsatira MCP ali ndi ufulu wochita zionetsero ngati akutsatira ndondomeko.

“Pali nkhani zina zomwe oweruza akaziona kuti n’zofunika bwalo

lapadera, amazitumiza kwa mkulu wa makhoti yemwe amaziunikanso payekha ndipo akakhutira, amakhazikitsa khoti la oweruza osachepera atatu omwe amaweruza nkhaniyo,” watero Kanyongolo.

Wachiwiri woyang’anira za kampeni mu MCP George Zulu yemwenso ndi phungu wa chipanicho kumwera cha kummawa kwa mzinda wa Lilongwe adati gululo lidzachoka ku Capital Hill Mutharika akadzatula pansi udindo.

“Akhoti ali ndi njira zawo zomwe amatsata pankhani zoterezi, alekeni azigwira ntchito yawo. Nafenso kuno tikutsata njira yathu ndipo tizibwera kuno tsiku lililonse la ntchito kuti kusapezeke munthu ogwira ntchito m’maofesi a boma,” adatero Zulu.

Kanyongolo adatsimikiza kuti nkhani yomwe ili mukhoti ndi zomwe akuchita otsatira chipani cha MCP ndi anzawo sizikukhudzana.

“Ndi nkhani ziwiri zosiyana, a khoti azipitiriza kuyendetsa nkhani yomwe ili mmanja mwawo. Awanso ndi ufulu wawo potengera malamulo kupanga chionetsero motsatira ndondomeko,” adatero Kanyongolo.

Koma mkulu woyang’anira zofalitsa nkhani ku unduna wa zofalitsa nkhani Gedion Munthali adati ufulu onena zakukhosi sukukhudzana ndi kutseketsa maofesi a boma chifukwa izi zikutanthauza kuimitsa boma, kusokoneza anthu osalakwa ndi kuononga katundu wa boma.

“Kuimitsa ntchito za boma, kuzunza anthu osalakwa, kugenda galimoto ndi kuphwanya katundu wa m’maofesi sizikukhudzana ndi kunena za kukhosi. Uwu ndi uchigandanga,” adatero Munthali.

Padakalipano landuwo uweruzidwa ndi Healey Potani, Michael Tembo, Ivy Kamanga, Dingiswayo Madise komanso Redson Kapindu. Aliyense akhala ndi chigamulo chake koma onse adzabwera pamodzi ndi kukhala ndi chigamulo chimodzi.

Related Articles

Back to top button