Chichewa

Chenjerani pokolola

Listen to this article

Mbewu ya chimanga nayo imafuna kuyichengetera nthawi yokolola kuti zokolola zikhale zochuluka ndi zopatsa kaso.

Wachiwiri kwa mkulu woona za kafukufuku wa mbewu ku Bvumbwe Research Station, Frank Kaulembe akuti nankafumbwe amaononga ngati alimi akolola chimanga chawo mochedwa kapena mofulumira.

Namkafumbwe amachecheta mosavuta chimanga chokololedwa mofulumira

Mwachitsanzo, iye adati kukolola mbewuyi isadaume,  mlimi akaiyanika imafota ndipo zotsatira zake nankafumbwe amaboola mosavuta.

“Mlimi akaichedwera, nankafumbwe wamkulu amayamba kuionongera kumunda komweko,” iye adatero.

Iye adaonjeza kuti kukolola chimanga chosauma nthawi yoyanika chimakumana ndi  ndi mavuto monga kunyowa ndi mvula yowaza komanso kukachita chifunga m’mawa, chimayamwa chinyontho mapeto ake chimachita chukwu,” iye adatero.

Pothirirapo ndemanga pa zomwe adayankhula Kaulembe, Paul Fatch, mphunzitsi wa kunthambi ya za ulangizi ya ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar), adati chimanga chimayenera kukololedwa chikakhwima komanso kuuma bwino ndipo chizindikiro chake n’choti chimaloza pansi.

“Pomwe, chimanga chimakhala chaumiratu ndipo kutonola chochepa ndi kuchiponya pansi chimachita phokoso,” iye adatero.

Ngakhale izi zili chomwechi, Fatch adati madera ena amayenera akololebe mwachangu kuopetsa akuba, chiswe komanso makoswe kotero alimi oterewa amayenera akachiumitse akafika nacho kunyumba pogwiritsa ntchito nkhokwe zoumitsira kapena dzuwa.

Kaulembe adafotoza kuti mlimi sakuyenera kulowa m’munda ndi kuyamba kukolola chimanga tsiku lomwe  kwachita mitambo ndipo kukuonetsa kuti nthawi ina iliyonse kukhoza kugwa mvula.

Iye adati chimanga chikanyowa ndi mvula chimachita chukwu.

Kaulembe adati ngati nthawi yokolola yafika koma kunja kukugwabe mvula, mlimi ayenera kuthandizira chimanga chomwe sichidaloze pansi kuti chitero ndi cholinga choti madzi asalowe m’chimanga muja koma azingotsetsereka kufikira ataona kuti mvula yaleka.

“Ichi nchifukwa chake kale makolo ankasanja chimanga chawo m’nkhokwe molozetsa pansi kotero ngakhale mugwere mvula, sichimaonongeka,” iye adatero.

Kuonjezera pa nankafumbwe yamwe amatha kuyamba kuononga chimanga chikakhalitsa m’munda,Kaulembe adati alimi asamakolole mochedwa kwambiri kuopetsa  chiswe ndi moto olusa.

“Pokolola, mlimi aziona pomwe akuika chimanga chake chifukwa chikakhala pafupi ndi chulu, chimagwidwa ndi chiswe komanso akaika pachidikha, chinyontho chimaononga,” iye adatero.

Mlimi wa chimanga m’boma la Salima Matiyasi  Banda adati saphuphulumira kukolola chimanga chake chifukwa amafuna kuti chiumiretu, akangofikira kutonola, kuthira mankhwala ndi kuchisunga.

“Ndidaona kuti kuyanika ndi ntchito ina yolemetsa yapadera kotero ndimangochisiya m’munda momwemo kuti chiumiretu.

“Ndimakolola pokhapokha makoko ake akamaoneka ouma kwambiri,” iye adatero.

Mlimi wina wa m’boma la Lilongwe Dust Chikumbutso  adati amakolola mwamsanga kuopetsa akuba.

Related Articles

Back to top button