Chichewa

Chigodola chavuta ku Nsanje

Listen to this article

 

Ng’ombe 70 m’boma la Nsanje zikutsalima, pamene 65 000 kumeneko zili pachiopsezo chotenga matenda a chigodola amene abonga m’bomalo.

Kafukufuku wa unduna wa zamalimidwe wa pa 8 January udapeza kuti matendawa abukanso m’bomali patangodutsa mwezi matendawa atazizira m’boma la Chikwawa.

Kutemera ng’ombe kudagundika ku Chikwawa
Kutemera ng’ombe kudagundika ku Chikwawa

Malinga ndi mkulu wa Shire Valley Agriculture Development Division (ADD), Jerome Nkhoma, panopa ndiye matendawa afika pagwiritse chifukwa sabata yathayi n’kuti ng’ombe 60 zitagwidwa koma pofika sabata ino ng’ombe zodwala zidafika pa 70.

Nkhoma adati ziweto za kudipi ya Bangula ku Magoti Extension Planning Area (EPA) m’bomalo ndi zomwe zili pampeni wotenga matendawa.

Padakalipano boma lalengeza kuti kuyambira tsopano, kupha nyama ya mbuzi, ng’ombe, nkhumba komanso nkhosa nkoletsedwa m’bomalo.

Kalata yomwe boma kudzera muunduna wa zamalimidwe idatulutsa ndipo idasayinidwa ndi mlembi mu undunawu Erica Maganga, idaletsa kugulitsa komanso kulowetsa kapena kutulutsa ziwetozi m’bomalo pokhapokha matendawa atakatuka.

Chibukireni matendawa m’boma la Chikwawa, ng’ombe 91 965 ndizo zidalandira katemera m’chigawo choyamba cha katemerayo.

Chikwawa ndilo lidali boma loyamba kubuka matendawa kutsatira kusefukira kwa madzi komwe kudachitika pa 12 January 2015.

Koma undunawu wati ntchito yolandiritsa katemera ku ziweto zomwe zakhudzidwa ndi matendawa kuli mkati.

Related Articles

Back to top button