Chikondi chidayambira kutchalichi

Mipingo ina ponyadira chipembedzo chawo imati ‘kupemphera ndi kwabwino kwatidziwitsa awa, awo ndi awo.’ Kukumana kwa mtundu womwewu kudasintha moyo ndi tsogolo la Elisha Mtambo ndi Menala Msiska womwe lero ndi banja.

Elisha yemwe amachokera m’dera kwa mfumu Mwenelupembe m’boma la Chitipa akuti adakumana ndi Menala wochokera m’dera la mfumu Kachulu m’boma la Rumphi m’chaka cha 2015 kutchalitchi ya CCAP ya Sinodi ya Livingstonia ku Area 24 mu mzinda Lilongwe.

Elisha ndi Menela paukwati wawo

Iye adati kupatula kukumana koyamba kutchalitchi, amakhulupilira kuti Mulungu ndiye adawalumikizitsa chifukwa atangowonana mitima yawo idadumpha mwachilendo pambuyo pake, adalonjerana n’kupatsana nambala za lamya pompo.

“Ambiri amadziwa kuti sichophweka kukumana ndi msungwana kapena  mnyamata koyamba n’kulankhulana naye pomwepo mpaka kupatsana nambala za lamya koma ndimo zidakhalira ndiye sindichotsera kuti dzanja la Atate lidayendapo,” adatero Elisha.

Naye Menala wati tsiku lomwe adakumana ndi Elisha kutchalitchi, adamva kugunda kwachilendo mumtima mwake koma pokhala msungwana adayesetsa kugwira thupi lake kuti asawonekere kuti adali kumva mwachilendo m’thupi.

“Munthu aliyense amazidziwa momwe amakhalira kapena kumvera nthawi zonse m’thupi mwake koma patsikuli, ndithu ndidamva mwachilendo makamaka momwe mtima wanga umagundira,” watero Menala.

Elisha wati kuchoka tsiku lokumanalo, awiriwa adakhala miyezi itatu akungocheza palamya kudikira tsiku lomwe onse adakhutira wina ndi mnzake.

“Tsiku lomwe ndidamufunsira, adaseka n’kundifunsa kuti ndidaganiza bwanji potenga nthawi yonseyo. Chilungamo chidali chakuti ndinkafufuza kaye za khalidwe lake,” adatero Elisha.

Iye wati atapereka yankho lakelo, adadzidzimuka Menala naye atamuuza kuti adagwa m’chikondi kalekale tsiku la kukumana kwawo koma sadafune kuonetsera ndipo pamiyezi itatu yomwe amangochezayo, nayenso amafufuza mbiri ya Elisha.

Ngakhale onse adali atamasukirana, Menala sadavomere kutomera kwa Elisha ndipo adamuuza kuti adzamuyankhabe akamaliza kulingalira za mawuwo.

“Ndidavomera maganizo akewo koma eeeeh! adandiyika mundende ya malingaliro usiku ndi usana. Adandilora pakutha pa mwezi wachiwiri, pemene ine ndinkati zanga zada,” Elisha adafotokoza.

Chibwenzi chitayamba mu 2015, akuti awiriwa adagwirizana zoti adzamanga ukwati m’chaka cha 2018 ndipo chibwenzicho chidayenda bwino kwa zaka zitatu zomwe amakonzekera ukwati wawo omwe adamanga pa 7 July 2018 patchalitchi yomwe adakumanirayo.

Menala wati Elisha ndi mwamuna wachikondi, wodziwa kusamala banja lake, woopa Mulungu komanso wopereka chilimbikitso pa nthawi yakufooka muuzimu ndi muthupi kotero kuti amayamika Mulunguyo pomupatsa mwamuna wotero.

Elisha naye adatsindika kuti banjalo adakonza yekha Mulungu, ndipo awiriwo sangasiyane.n

Share This Post