ChichewaEditors Pick

CHIPWIRIKITI MUMPINGO WA ABRAHAMU KU BANGWE

Listen to this article

Nkhosa zakana kuwetedwa. Akhristu ampingo wa Abrahamu ku Bangwe mumzinda wa Blantyre aimika Bishopu wawo, ati chifukwa chokana kuti nkhosa zake zimudzudzule pankhani zosiyanasiyana.

Mondiwa kulowa pakhomo la kachisi wa Abrahamu
Mondiwa kulowa pakhomo la kachisi wa Abrahamu

Akuti Akhristu mumpingowo adanyanyuka pomwe mkangano pakati pa bishopuyo, Justin Chome, ndi nkhosa zake zidafika kubwalo la nyakwawa Mondiwa m’deralo.

Malinga ndi mbusa wa pampingopo, Frank Somba, Akhrisituwo akhala asakutolerana ndi bishopuyu chifukwa ati samamva chidzudzulo.

“Pali nkhani zambiri ndi zina zomwe sindinganene. Tikawadzudzula amadana nazo ndipo amati bishopu sadzudzulidwa chifukwa Mulungu ndiye akawadzudzule,” adatero Somba.

Izi akuti zidakwiyitsa Akhrisituwo ndipo limodzi ndi mbusayo komanso akulu a mpingo adagwirizana zoimitsa mbusayu kuyambira pa May 6 mpaka September chaka chino.

Koma Msangulutso utafunsa bishopuyo ngati Akhrisituwo akunena zoona, iye adangoseka, amvekere: “Ha-ha-haaa! Nzovuta kulankhulapo, koma panopa nkhaniyo ikukambidwabe.”

Koma iye adavomerezadi kuti kumpingoko kuli kavuwevuwe.

“Nzoonadi kudali chipwirikiti moti panopa ndaima kaye kupitako. Sindidayambitse mpingo wina kapena kulowa wina, koma ndapuma kaye,” adatero Chome.

Bishopuyu atangoimitsidwa, nkhaniyo akuti idafika kwa pulezidenti wa mpingowo Akasani Wonderford Zunga amene adalembera kalata mfumu Mondiwa kuti alange nkhosazo.

Zunga adatsimikizira Msangulutso kuti adalembera kalata mfumuyo koma sadathandizidwe.

“Ndidalemberadi mfumuyo kuti iwalange [Akhrisituwo] koma ndaonanso kuti padalakwika. Komabe ndidatero chifukwa Akhrisituwa amazitenga mwa kuthupi pamene nkhaniyo ndi ya uzimu. Nawonso amfumuwo sadatithandize kuzimitsa motowo,” adater Zunga.

Zunga adati mpingo wawo uli ndi malamulo ake koma sadafune kutsatira malamulo chifukwa choti Akhrisitu amachita zinthu mwa kuthupi.

“Taonadi kuti nkhaniyi isokonekera ndiye panopa ndafika mumzinda wa Blantyre kuti tikambirane bwinobwino ngakhale zinthu zasokonekera kale,” adatero Zunga, amene akuti mpingowu udachokera m’boma la Ntcheu komwenso iye akukhala.

Mondiwa adati adali wodabwa kulandira kalata yoti alange Akhristuwo pamene mpingo uliwonse umakhala ndi malamulo ake.

“Ndidawaitana kuti abwere koma chodabwitsa [n’choti] iwo sadabwere ndipo amene adabwera ndi bishopu ndi Akhrisitu ake,” adatero Mondiwa amene akuti sadapereke chigamulo.

“Mpingo ulionse umakhala ndi malamulo ake. Ine ndinadabwa kuti nchifukwa chiyani nkhaniyi akuti ibwere kubwalo langa pamene mpingo umakhala ndi malamulo ake?

“Poti akuluakulu a mpingowu sadafike, ndidawalangiza kuti bishopuyu atsate zomwe Akhrisituwo akunena,” adatero Mondiwa.

Koma bwalolo litasonkhana, Akhristituwo adakakamira chigamulo chawo kuti bishopuyu apume kaye. “Sitikuti asiye mpingo kapena kuti ifeyo tamuchotsa, koma kuti asagwirenso ntchito yawo [akhale membala basi],” adatero Somba.

Kumbali ya momwe mpingo ukuyendera, Somba adati chiperekereni chigamulocho, mpingowu ukuyenda bwino ngakhale bishopuyo sakupitako.

“Kuchokera tsiku lomwe tapumitsa bishopuyu, Akhrisitu ayamba kubwera mwaunyinji komanso mokondwa ndipo onse amene adasiya kupemphera nafe abwerera. Zinthu zili bwino panopa,” adatero Somba akusekerera.

Malinga ndi mfumu Mondiwa, mpingowu udadza m’mudzimo m’chaka cha 1972. 

Related Articles

Back to top button
Translate »