Nkhani

Chisiki: Mchezo wa amayi

Listen to this article
Chikondano: Amapatsana zinthu mwachinsinsi
Chikondano: Amapatsana zinthu mwachinsinsi

Pamoyo wathu pali njira zambiri zomwe timalumikizirana pophunzitsana, kugawana nzeru ndi kuunikirana. Umu ndimo moyo ulili. Ngakhale izi zili choncho, ambiri amaona ngati okhala nawo pafupi ndiwo angakhale abwenzi awo, koma maganizo oterewa akutsutsidwa ndi mchezo wa amayi womwe amautcha chisiki. Ndidacheza ndi Miriam Chikondano, yemwe akulongosola za chisiki motere:

Moni mayi ndipo ndikudziweni.

Zikomo, bambo. Ine ndili bwino ndipo dzina langa ndine Miriam Chikondano wam’mudzi mwa Chimoka ku Lilongwe. Ndili pabanja ndipo ndili ndi ana 4—anyamata atatu ndi msungwana mmodzi, mzime.

Mudapalanako ubwenzi ndi mayi mnzanu?

Kwabasi, moti padakalipano ndili ndi abwenzi achizimayi ambiri zedi omwe ndimagawana nawo nzeru ndi kucheza nawo.

Ubwenzi woterewu mumawuona bwanji?

Choyamba ndimasulire tanthauzo la mawu akuti ubwenzi chifukwa masiku ano anthu amaganiza mothamanga ndiye ena amadzayamba kutanthauzira mawuwa mwawomwawo. Mawu akuti ubwenzi amatanthauza chinzake pakati pa anthu awiri kapena kuposerapo. Mukafunsa za mmene ndimauonera ubwenzi woterewu yankho langa ndi lakuti ndi njira imodzi yabwino kwambiri yomwe anthu amagawanirana nzeru, kulangizana ndi kulumikizana pankhani zosiyanasiyana.

Kodi mgwirizano wa amayi umatchedwa kuti chiyani?

Mgwirizano wa amayi umatchedwa kuti chisikileti koma mwachidule amangoti chisiki ndipo mzimayi mmodzi amatha kukhala ndi zisiki zingapo panthawi imodzi popanda vuto kapena madandaulo alionse.

Dzinali limachokera pati?

Dzinali lisakuzunguzeni, ayi, limachokera pa mawu Achingerezi oti ‘secret’ koma ndi longofuna kusiyanitsa maubwenzi ena ndi ubwenzi umene tikukambirana panowu. Dzinali limabwera potengera zomwe zimachitika paubwenziwo. Apa ndikutanthauza zomwe mayi ndi bwenzi kapena abwenzi ake amapangirana paubwenzi wawo.

Mungatambasule zomwe zimachitikazo?

Panthawi ya ubwenziwo amayi amagulirana mphatso zosiyanasiyana mwamseri n’kumapatsana mokhala ngati mobisa zija m’Chingerezi amati ‘secret’ monga ndanena kale, ndiye pofuna kusazungulira amangoti chisiki basi.

Chisiki chimayamba bwanji?

Pali njira zambiri zomwe chisiki chimayambira koma mfundo yaikulu yagona pakuti anthuwa amakhala paubwenzi. Chisiki china chimayamba chifukwa anthu amachokera kumodzi, china chimayamba chifukwa chakuti anthu amayendera limodzi kapena adakumana kumalo kapena kuzochitika zina zake monga kutchalitchi, kumpalano wa magule, kumsonkhano ndi malo ena.

Ndiye zimayamba bwanji?

Ngati anthu agwirizana magazi amatha kukambirana kuti ayambe chisiki koma nthawi zina wina amangoyamba kutumizira mnzake mphatso kenako winayo amabweza basi chisiki chayamba chikatero.

Phindu lake ndi lotani?

Pali phindu lalikulu kwambiri, makamaka pamoyo wa munthu wamayi. Amayi amakhala ndi nkhawa komanso milandu yambiri mumtima kuposa abambo ndiye ngati mzimayi alibe mnzake womukhuthulira nkhawa ndi milandu yotere, moyo wake umakhala wokwinyirira ndiponso zinthu siziyenda koma akakhala ndi mnzake ngati siki wake amatha kukhuthulira khawa ndi mavuto otere kwa mnzakeyo, mtima n’kumapepuka.

Basi phindu lake n’kukhuthula nkhawa ndi mavuto?

Ayi, chomwe ndikutanthauza n’chakuti pamakhala nkhawa ndi madandaulo ena ofunika kutanthauziridwa kapena kulimbitsidwa mtima ndiye amayi awiriwo pausiki wawo amakhala pansi n’kukambirana za nkhani ngati zimenezi nkuthandizana nzeru kuti zinthu ziziyenda m’ndondomeko yake.

Nanga chisiki chimatha kapena n’chamuyaya?

Chikhoza kutha malingana ndi zifukwa zake koma osangoti kwacha mmawa basi n’kumati ndikuthetsa chisiki popanda chifukwa kapena mlandu uliwonse. Chifukwa chachikulu chagona pakusungirana chinsinsi monga ndanena kale kuti amayi omwe ali pachisiki amatha kuuzana za mavuto osiyanasiyana okhudza moyo wawo ngakhalenso a m’banja. Ndiye ngati wina akunka nalengeza za mavuto a mnzake chisiki sichingapitirire chifukwa palibenso ulemu kapena chinsinsi.

Mungawauze chiyani amayi za chisiki?

Mawu ndiwochepa. Mpofunika kusamala posankha bwenzi la chisiki basi. Ndi bwino ukaona kuti mnzako ali ndi chidwi choti mukhale pachisiki kumufufuza bwino lomwe kupewa kuti mudzayambane n’kudana patsogolo.

Related Articles

Back to top button