Nkhani

DPP igwa pa chisankho ku Mzimba

Listen to this article

Katswiri pa ndale, mkulu womenyera ufulu wachibadwidwe, komanso anthu ku Mzimba ati kumbwita kwa chipani cha DPP pamasankho achibwereza ku Mzimba n’chisonyezo kuti anthu sakufuna chipanichi potengera zomwe chidachita panthawi yomwe chidali paulemerero.

Ndemangazi zadza pomwe chipanichi chataya mipando iwiri pa chisankho cha chibwereza.

Kudera lapakati m’bomalo, mpando wapita kwa phungu woima payekha, Joseph Mabvuto Kachali yemwe adasomphoka ku chipani cholamula cha People’s potsatira kusamvana pa chisankho cha chipani cha chipulula ku chipanicho.

Kudera la kummwera chakuzambwe, mpando wapita kwa Raymond Nkhata wa chipani cholamula cha People’s (PP).

Koma mneneri wa DPP, Nicholas Dausi, wati anthu asasase chipanichi ngati msabwe, ati chipanichi chikonza monse moyenera polunjika ku chisankho cha 2014 pomwe ati chidzatengenso boma.

Anthu sangakhumbirenso DPP

Koma apa Kanyongolo wati Amalawi sangakhumbirenso kuvotera DPP chifukwa cha zomwe zidachitika mu ulamuliro wake.

“Uwu ndi uthenga kuti anthu sadaiwale zovuta zomwe adaziona muulamuliro wa chipanichi. Anthu adaphedwa pazionetsero komanso nkhani za [kuphedwa kwa] Robert Chasowa.

“Anthu angachikhululukire ngati chitapepesa Amalawi, osati kumangolankhula, koma kutchula zomwe adalakwitsa,” adatero mkuluyu yemwe adalangiza chipani cha PP kuti chisatayirire chifukwa chapeza mpando umodzi.

Naye Mayaya adati Amalawi akufuna kusintha kotero n’chifukwa sakufunanso kuti abwezeretse chipani cha DPP pamipandoyo.

“Zomwe DPP idachita kumapeto n’zomwe anthu akukumbuka,” adatero Mayaya yemwe adaunikira PP kuti isakomedwe chifukwa mpando umodzi sutanthauza ulemerero wotheratu.

Koma wachiwiri kwa mneneri wachipani cha PP, Ken Msonda wati kupata mpando kukusonyeza kuti anthu akukondwera ndi ulamuliro wa Banda.

“Anthu sakuiwala zomwe boma la mayi Joyce Banda likuwachitira komanso mudziwe kuti phungu yemwe wapambana ngati woima payekha wachokera ku PP.

“Iyi ndi nkhani yabwino kuchipani chathu,” adatero Msonda, uku akulonjeza kuti boma lizichita zomwe anthu akufuna.

Joyce Phiri wa m’mudzi mwa Manyamula kwa T/A Mbelwa m’bomalo wati akusangalala ndi momwe masankho ayendera.

Anthu samabwereza phungu

Iye adati kumeneko anthu samabwereza phungu, maka ngati sadawapindulire, kotero akukhulupirira kuti aphungu omwe asankhidwawo awathandiza.

Gibson Ngulube wa m’mudzi mwa Mbalachanda kwa T/A Mpherembe m’bomalo wati boma lidzimvera zofuna za anthu.

Iye adati kumeneko anthu adasankha Kachali kuti adzawayimire koma a PP adatsata zofuna zawo.

“Tavotera yemwe timafuna. Apa boma liphunzire kumvera oponya voti,” adatero mkulu wa bizinesiyu yemwenso akuti adakavota.

Kummwera cha kumzambweko chisankho chatsatira kusankhidwa kwa Khumbo Kachali kukhala wachiwiri kwa pulezidenti. Wolembetsa adalipo 41 740 ndipo omwe akaponya voti ndi 20 567.

Woima payekha Baxter Manzunda wapeza mavoti 219, Ronald Chavula wa DPP adapeza 3 210, Raymond Nkhata wa PP adapeza 9654 ndipo James Nthara woima payekha adapeza mavoti 4636.

Kudera lapakati m’bomalo chisankho chakhalapo kaamba ka imfa ya phungu wachipani cha DPP, Donton Mkandawire. Wolembetsa adali 34 816 koma omwe aponta voti ndi 18 007.

Kachali mavoti 9412, Aram Beza wa PP yemwe wakolola mavoti 8154, Owen Mkandawire wa DPP 2313, Dennis Kandodo Mvula woima payekha 55, Enita Njolwa wa Aford 341 ndi Bonfacia Nguluwe wa New Rainbow Coalition (NARC) 18.

Related Articles

Back to top button