DPP ikutolera Nambala zovotera

Ziyangoyango pa chisankho! Anthu ena achipani cha DPP akuti akutolera nambala za ziphaso za unzika, komanso zovotera kwa anthu amene adalembetsa.

Izi zikuchitika ku Phalombe, Mulanje, Balaka, Ntcheu, Kasungu, Mchinji ndi Rumphi.

Anthu ena akulemba nambala za ziphaso ngati izi

Ngakhale mlembi wa DPP, Greselder Jeffery ndi mneneri wake Nicholas Dausi adakana kuikapo mlomo pa nkhaniyi, mdindo wina m’chipanicho wauza Tamvani Lachitatu kuti iyi ndi njira yomwe akhazikitsa kuti apeza mavoti ambiri pachisankho chikudzachi.

Lolemba Enelesi Nyandula wa m’mudzi mwa Bamba m’dera la mfumu yaikulu Phambala ku Ntcheu adauza mtolankhaniyu kuti achipani cha DPP adabwera m’mudzi mwawo kudzatolera nambalazo.

“Akufuna nambala za ziphaso zathu, kodi tiwapatse?” adafunsira nzeru Nyandula. “Akuti n’zokhudzana ndi zisankho zikudzazi, ena apereka kale nambala zawo.”

Iye adati ali ndi mantha kuti mwina sadzapeza mwayi wodzavota poganizira kuti mwina voti yake yaponyedwa kale.

Gavanala wa DPP m’chigawo cha kummwera m’bomalo, Jeremiah Lilani, adavomera kuti akutolera nambalazo popeza wauzidwa ndi akulikulu kwa chipani chawo.

Lilani adati DPP ikutolera nambala za anthu omwe akonzekera kudzavotera chipanicho pa May 21.

“Tikufuna tidziwe amene adzativotere. Tikatolera nambalazo tikumawaika m’maeliya momwe akuyenera kukhala,” iye adatero.

Titamufunsa kuti adzadziwa bwanji kuti munthuyo wavotera chipanicho, gavanalayo adati ali ndi chikhulupiriro choti anthuwo sadzawaputsitsa podzavota.

“Kungotolera nambala kokhako aliyense azidziwiratu kuti chipani chovotera ndi cha DPP ndipo tikukhulupirira sadzatipusitsa,” adatero Lilani.

Bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) ladzudzula mchitidwewu.

Mmodzi mwa akuluakulu a MEC, Jean Mathanga Lachitatu adati ofesi yake yamva zoti anthu ena akutolera manambala za anthu, koma palibe amene wadandaula ku bungwelo.

Iye adati kutenga nambala ya chiphaso cha munthu wina ndi mlandu malingana ndi gawo 24 ndime 3, 4 ndi 5 ya malamulo oyendetsera zisankho a dziko lino ndipo wopezeka wolakwa ayenera kukaseweza zaka 7 m’ndende.

“Koma palibe mlandu kungotenga nambala ya chiphaso. Komabe funso ndi loti kodi akufuna akatani nazo? Ukuku ndi kungosokoneza mitu anthu odzavota ndipo tikuyenera kuchitapo kanthu msanga,” adatero Mathanga.

Iye adati aliyense amene nambala yake yatengedwa, chiphaso chake chidataika kapena kupsa, asadandaule chifukwa adzavotabe.

“Uthenga umveke kuti nonse amene ziphaso zanu adakutengerani, zidasowa kapena nambala yanu atenga, muli ndi mwayi wodzavota ndipo patsikulo dzapiteni mukavote,” iye adatero.

Mathanga adati aliyense amene watenga chiphaso kapena nambala ya mnzake sangathe kuigwiritsa ntchito povota.

Vutoli lafalikira paliponse

Sibongile Machinjiri wa m’mudzi mwa Lunguzi m’dera la mfumu yaikulu Lundu ku Blantyre adati adauzidwa kuti apereke nambala yake ya unzika, koma sadamufotokozere chifukwa chake.

“Adatenga nambala ya chitupa changa ndipo poyambapo amati atipatsa chakudya, koma mpaka lero palibe chomwe chachitika,” adatero Machinjiri.

Enock Mangola, wa zaka 70 wa m’mudzi mwa Mishoni, m’dera la mfumu yaikulu Mabuka ku Mulanje adati nambala za anthu ena zatengedwa kale m’deralo.

“Sitikudziwa chomwe akufuna apange nazo, koma zayamba kutiopsa,” adatero Mangola.

Mkulu wa zophunzitsa anthu m’bungwe la Nice m’chigawo cha kummwera Enoch Chinkhuntha adati bungwe lawo lamva za nkhaniyo ndipo akufufuza.

“Tikudziwa kuti anthu ena akuchita izi pongofuna kuzunguza ovota.

“Akufuna kuti aziona ngati wina akatenga nambala yawo ndiye kuti adzadziwa momwe wavotera. Ayi voti ndi ya chinsinsi,” adatero Chinkhuntha.

Iye adati mwa ena amene akhala akutolera nambalazo ndi mafumu. “Uwu ndi mlandu ndipo sitikugona, tikufufuza izi,” iye adanenetsa.

Malinga ndi Moir Walita Mkandawire yemwe amatsogolera bungwe loima palokha ku Rumphi, izi zikuchitika ku Mlowe, Chiweta, Zunga ndi Old Salawe.

Iye adati nkhaniyo itamveka adakadziwitsa bungwe la Nice, koma mpaka lero palibe chachitika.

Mkulu wa Nice m’boma la Rumphi, Mollen Zgambo, adati akufufuza umboni kuti ayitengere pena nkhaniyi.

Gulupu Zinkambani ya ku Nkhamenya m’boma la Kasungu idati  mchitidwewu adayamba kalekale m’deralo.

Iye adati mafumu adakumana n’kukambirana za mchitidwewu ndipo adagwirizana zothana ndi wina aliyense wopezeka akutolera nambala za anthu.

Mariko Zinenani wa m’dera la mfumu Kalumo ku Ntchisi adati izi zikuchitika, koma sakudziwa chipani anthu omwe akuchita izi.

“Anthuwo amati tipereke nambalazo ponena kuti akufuna atilembe kuti tilandire zipangizo zotsika mtengo, koma mpaka lero sitidaone yankho lake,” adatero Zinenani.

Bungwe la MEC lidalemba anthu 6.8 miliyoni kuti ndiwo akaponye voti.

Achinyamata-alipo 3.7 miliyoni pamene 2.1 miliyoni ndi amayi komanso `1.6 miliyoni abambo.-Ena amene athandizira nkhaniyi ndi Kondwani Kamiyala, Martha Chirambo ndi Steven Pembamoyo. n

Share This Post