Nkhani

Escom isayerekeze kukweza magetsi—Banda

Listen to this article
Makina amagetsi a Escom
Makina amagetsi a Escom

Kutsatira zomwe mkulu wa zachuma kukampani ya magetsi m’dziko muno ya Escom Delano Ulanje adauza wailesi ya MBC kuti bungweli likweza magetsi posakhalitsa, mkulu wa bungwe loona za ufulu wa anthu la Malawi Watch Billy Banda wati kampaniyi losayesere zokweza magetsi.

Lachinayi Ulanje adakanira The Nation kuti sangabwerezenso mawu amene adalankhula pa MBC kotero tilankhule ndi mneneri wa bungweri.

Koma mneneri wa bungweli George Mituka adati sizoona kuti pali chikonzero chokweza magetsi.

Ngakhale pali kukanirana kotero komabe Banda wati ndi chipongwe kuti bungweri likweze magetsi pamene anthu akuvutika ndi nkhani zachuma.

“Chuma sichidapole, ngati bungweli lingakweze magetsi ndiye kuti zonse zikwera mtengo. Boma likuyesetsa kuti zinthu ziziyenda bwino pamene iwo akufuna kukweza magetsi. Ndiye kuyenda bwino kwake kuti?

“Ngati atero ndiye kuti akusemphana ndi zomwe boma likuchita kuti anthu azisangalala ndi momwe zinthu zikuyendera. Ife ngati amabungwe tikuti ayi,” adatero Banda.

Banda adati sanganeneretu chomwe bungwe lake lichite ngati Escom ikweze magetsi koma wati adzawona chomwe angachite.

Kuyambira May chaka chatha magetsi akwera katatu zomwe zachititsa kuti zinthu zikwere mitengo.

Izi zikuchitika pamene magetsi akungozima m’dziko muno.

Sabata zingapo zapitazo, ena adadzudzula kampaniyo kuti ikuononga ndalama pogula galimoto za K1.4 biliyoni ndipo ena akhala akudandaula ndi kuzimazima kwa magetsi.

Related Articles

Back to top button