Chichewa

Evance Masina: Mapanga awiri samuvumbwitsa

Listen to this article

Pali mwambi woti ndigwire uku ndi uku pusi anagwa chagada. Penanso amati mapanga awiri avumbwitsa, kutanthauza kuti ndibwino kuchita chinthu chimodzi panthawi imodzi kuti zikuyendere. Koma Evance Masina akutha bwanji sukulu ndi kusewera mpira m’kalabu komanso n’kumachita bwino m’zonse? DAILES BANDA adacheza naye motere:

Akufunitsitsa atadzasewerapo kunja
Akufunitsitsa atadzasewerapo kunja

Ndikudziwe mnyamata.

Ndine Evance Masina wa zaka 18. Ndimachokera m’mudzi mwa Ntamba T/A Nkalo m’boma la Chiradzulu. Ndine wachinayi m’banja la ana asanu. Pakadalipano ndikuphunzira pasekondale ya Moyale ku Mzuzu komwe ndili mu Fomu 3.

 

Umatchuka kwambiri chifukwa chosewera mpira, kodi udayamba bwanji kusewera?

Mpira ndidayamba kalekale ndili mwana koma zenizeni ndidayamba kusewera wa Under-12. Ndinkasewera timu ya Young Buffalo ya ku Mzuzu konkuno. Nditadutsa zaka 12 ndidapitiriza kusewera ku Young Buffalo m’timu ya Under-14. Padachitika zovuta zinazake zomwe zidandichititsa kuti ndikayambe kusewera ku Chiputula United m’timu ya Under-20. M’chaka cha 2014 ndi pomwe ndidayamba kusewera mutimu ya Fish Eagles komwe ndili mpaka pano. Timuyi ikutsogola muligi ya chikho cha FMB ku Mzuzu kuno ndi mapointi 38.

 

Wachinyako zigoli zingati kutimiyu?

Ndachinya zigoli 26 mumasewero okwana 14 m’chikho chimenechi.

 

Chisangalalo chako ndi chotani pokhala amene wachinya zigoli zambiri m’ligiyi?

Ndine wosangalala kwambiri chifukwa si chinthu chapafupi kuchita zoterezi. Pokhala mwana wasukulu zochita zimandichulukira. Ichi ndi chinthu chomwe ndakhala ndikufuna nditakwaniritsa m’moyo mwanga ndipo ndine wokondwa kuti ndachikwaniritsa.

 

Umakwaniritsa bwanji kupanga za sukulu ndi za mpira?

Ndimayesetsa kupanga pulani momwe ndichitire tsiku ndi tsiku ndi cholinga choti ndizitsatira bwinobwino zomwe ndikufunika kuchita kupewa kusokoneza zochita zina.

 

Masomphenya ako?

Chachikulu chomwe ndimafuna nditakwaniritsa ndi kusewera mutimu yaikulu m’Malawi muno monga Silver Strikers, komanso mutimu ya dziko. Ndimafunitsitsanso nditadzasewerako mutimu yakunja.

 

Osewera amene amakusangalatsa ndi ati?

Ndimasangalatsidwa ndi maseweredwe a Chawanangwa Kaonga wa timu ya Silver Strikers komanso James Rodriguez amene amasewera mutimu ya Real Madrid.

 

Umakonda kuchita chiyani ukakhala sukusewera mpira?

Ndimakonda kuonerera mafilimu ndi kumvetsera nyimbo.

 

Achinyamata anzako uwalangiza zotani?

Alimbikire pachilichonse kuti adzakhale opambana.

Related Articles

Back to top button