Nkhani

Flames inyamuka mawa

Listen to this article

 

Timu ya Flames ikunyamuka mawa m’dziko muno ulendo ku Tanzania kukaswana ndi timuyi masewero amene alipo Lachitatu pa 7 October.

Iyi ndi ndime yachipulula mumpikisano wa Fifa 2018 World Cup ndipo masewero achibwereza ali Loweruka likudzali pa Kamuzu Stadium.Flames_chad

Malinga ndi mlembi wa Fam Sugzo Nyirenda, osewera akumana cha m’ma 6:00 madzulo ano kuchoka kosewerera makalabu awo.

Timu ikanyamukira ku Lilongwe nthawi ikamati 7:30 mmawa. Masewerowa akachitikira pabwalo la Benjamin Mkapa ndipo adzayamba 3:00 masana nthawi ya ku Malawi kuno.

Mtawali adatenga osewera monga Simplex Nthala, Bighton Munthali, Stanley Sanudi, John Lanjesi, Yamikani Fodya, Miracle Gabeya, Pilirani Zonda, Limbikani Mzava, Isaac Kaliati, Chimango Kaira, Robert Ng’ambi, Micium Mhone, John CJ Banda, Levison Maganizo, Gerald Phiri Jnr, Dalitso Sailesi, Manase Chiyese, Robin Ngalande, Chawanangwa Kaonga ndi Frank Gabadinho Mhango.

Related Articles

Back to top button