Nkhani

Gawo 65 yazunguzanso mitu aphungu

Mpungwepungwe wabukanso ku Nyumba ya Malamulo pomwe pali kuponyerana Chichewa pakati pa aphungu achipani cha DPP ndi aphungu omwe adachoka kuchipanichi kukakhala mbali ya boma pa za Gawo 65 la malamulo oyendetsera dziko lino.

Gawoli limati phungu amene wachoka chipani chake, n’kulowa gulu lina lomwe ndi la ndale, adzachotsedwa pampandowo ndpo m’dera mwawo mudzachitike chisankho.

Gawoli lidavutanso muulamuliro wa chipani cha DPP pomwe mtsogoleri wa chipanichi, Bingu wa Mutharika mu 2005 adachoka kuchipani cha UDF chomwe adapambana nacho pamasankhoa 2004 ndikukayambitsa chipani chake cha DPP.

Masiku apitawa, aphungu a DPP anadandaulira sipikala wa nyumbayo, Henry Chimunthu Banda, pa za aphungu awo omwe adakwawira kumbali ya boma ponena kuti Gawo 65 la Malamulo adziko lino likuyenera ligwire ntchito yake.

Aphungu oposa 40 adakwawira kumbali ya boma kuchoka kuzipani zawo.

Lachinayi pa 21, Chimunthu Banda adapempha aphungu achipani cha DPP kuti apereke umboni kuti aphungu ena alowa mbali ya boma.

Lachisanu pa 22 sipikalayo adati apereka chigamulo chake koma izo sizidatheke kaamba ka chiletso chomwe phungu wa DPP kuchigawo chakumadzulo m’boma la Ntcheu yemwenso ndi nduna ya zamaphunziro, Chikumbutso Hiwa adakatenga kuletsa Chimunthu Banda kupereka chigamulo chake pa za gawo 65-lo.

Izi sizidakomere aphungu a DPP omwe adati apita kubwalo lamilandu kuti chiletsocho chichotsedwe.

Mtsogoleri wa aphungu a chipanicho m’nyumbayo, George Chaponda adauza Tamvani kuti akambirananso ndi sipikalayo pa nkhaniyo.

Koma T/A Chekucheku ya m’boma la Neno yati lamulo likuyenera kugwira ntchito yake mosazengereza.

“Aphungu amenewa amachita zofuna zawo ndiye apa tikuti lamulo ligwire ntchito. Kumudzi kuno kuli mavuto ambiri koma iwo akutsata zofuna zawo,” adatero Chekucheku.

Mu 2005, aphungu adachoka kuzipani zawo ndikukwawira kuchipani cha DPP.

Sipikala wa nyumbayo, Louis Chimango adalephera kugwiritsa ntchito gawolo chifukwa cha chiletso chomwe phungu wa DPP kuchigawo cha pakati m’boma la Zomba, Yunus Mussa adakatenga kubwalo lamilandu kuletsa sipikalayo kupereka gamulo lake.

Related Articles

Back to top button