Nkhani

Kafukufuku wa cashgate sadayankhe

Listen to this article

Mabungwe omwe si aboma ati zotsatira za kafukufuku wa kubedwa kwa ndalama za boma (cashgate) kulikulu la dziko lino zomwe boma latulutsa sabata ino zangokanda pamwamba pa nkhani zikuluzikulu zomwe Amalawi amayembekezera.

Mabungwewa ati imodzi mwa nkhani zikuluzikulu zomwe zotsatira za kafukufukuyu sizidachite bwino ndi kubisa maina a anthu komanso makampani omwe akukhudzidwa ndi nkhaniyi.

John Kapito, mkulu wa bungwe loona za anthu ogula ndi kugwiritsa ntchito katundu wosiyanasiyana, yemwenso amakonda kulankhulapo pankhani za mmene zinthu zikuyendera m’dziko muno, wati zotsatirazo zikadatchula maina a anthu ndi makampani okhudzidwa kuti anthu adziwe.

“Munthu aliyense yemwe akutsatira bwino za nkhaniyi akuyembekezera kudziwa anthu ndi makampani omwe adasakaza chuma chawo koma zotsatirazi zangokhazikika pa kuchuluka kwa ndalama zosokonekerazo ndi momwe zidasokonekerera basi zomwe anthu adamva kale,” watero Kapito.

Boma lidapereka mphamvu kukampani ya ku Britain ya Baker Tilly Business Services kuti ichite kafukufuku wakuya pankhaniyi ndipo idapeza kuti ndalama zonse zomwe zidasokonekera ndi K13.6 biliyoni.

Malingana ndi zotsatira zomwe zatulutsidwazo kampaniyi idalephera kuulutsa maina a anthu ndi makampani okhudzidwa poopa kusokoneza milandu ya nkhaniyi yomwe pakalipano ili kukhoti.

Pakadalipano milandu yokwana 70 ili m’mabwalo a milandu momwe anthu osiyanasiyana ogwira ntchito m’boma akuwafunsa kuti alongosole bwino za mmene adapezera chuma chankhaninkhani ndi ena omwe adapezeka ndi ndalama zambiri.

Nduna ya zachuma Maxwell Mkwezalamba wati kafukufukuyo sadalondole pandalama zomwe zidasokonekera ati chifukwa ochita kafukufukuyo adafukula mbali zina zomwe samayenera kukhudzako.

“Ndalama zenizeni zomwe zidasokonekera ndi K6.1 biliyoni osati K13.6 biliyoni monga mmene zotsatira za kafukufukuyu zikusonyezera. Akatswiri omwe amachita kafukufukuyu adapeza K13.6 biliyoni chifukwa adalowerera m’madera ena omwe samafunika kukhudzamo,” watero Mkwezalamba polongosola.

Kutengera nyuzipepala ya The Nation ya Lachiwiri lapitali akatswiri omwe adachita kafukufukuyu adzudzula banki yaikulu ya Reserve Bank of Malawi ndi mabanki ang’onoang’ono polephera ntchito yawo ndi kulekerera ndalama zambiri zikupita m’madzi.

Kafukufukuyu wati mwa maakaunti 554 a kubanki aboma akatswiri ochita kafukufukuyu adaloledwa kuunika maakaunti 11 okha zomwe mabugwe ati n’zogwetsa mphwayi kukhulupirira zotsatira za kafukufukuyo.

Mmodzi mwa akuluakulu a mabungwe omwe si aboma Lucky Mbewe wa bungwe loona kuti achinyamata akupatsidwa mphamvu zokwanira zotenga nawo mbali pachitukuko wati boma silikuonetsa chidwi pankhani ya kusokonekera kwa ndalamaku.

Iye wati ngati nzika za dziko lino, Amalawi ali ndi ufulu wodziwa chilichonse pankhaniyi ndipo wapempha kuti boma lisinthe mmene likutengera nkhaniyi ndi kupanga zakupsa kuti Amalawi akhale ndi chikulupiriro m’boma lawo.

 

Related Articles

Back to top button