Nkhani

Kapito adzudzula kukweza mitengo

Listen to this article

Patangotha sabata bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority (Mera) litakweza mitengo ya magetsi ndi mafuta agalimoto, madera ena maka kumidzi zinthu akuti zayamba kale kukwera mtengo.

M’maderawa, monga ku Chikhwawa, mitengo yogayitsira komanso maulendo a galimoto akuti yakwera kwambiri.

Kukwera mitengo kwa zinthuku kukutsutsana ndi zomwe bungwe la Mera, lomwe limayang’anira za magetsi ndi mafuta, lidanena kuti kukwera kwa mafuta ndi magetsi sikuchititsa kuti zinthu zikwere mtengo.

Bungweli lidakweza mitengo yogulira mafuta ndi magetsi Lachinayi sabata yathayi. Bungweli lidati kuyambira Lachisanu pa 9 Novembala, petulo azigulitsidwa pa K606.30 kuchoka pa K539.00 pa lita. Dizilo adati azigulitsidwa pa K509.90 kuchoka pa K434.30 pa lita.

Lidatinso mtengo wogulira magetsi wakwera kuchoka pa K16.05 kilowatt hour kufika pa K22.78 kilowatt hour.

Apa anthu ati boma litsitse mtengo wa mafuta ndi magetsi kapena lipeze njira zoti katundu yemwe wayamba kale kukwera mtengo atsike.

Anthuwa omwe ena ndi abizinesi ati ngakhale akuchita bizinesi komabe malinga ndi kukwera mtengo kwa zinthu kukhala kovuta kuti azipeza phindu pa zomwe akuchita.

Macleod Banda wa m’mudzi mwa Maide kwa T/A Maseya m’boma la Chikhwawa ndipo ndi mlimi wa mpendadzuwa akuti kumeneko zigayo ndi maulendo zakwera.

“Thini la malita 15 timagayitsa K120 koma pano lili pa K150. Izi ndi zigayo zoyendera magetsi. Tikafuna kulowa m’tawuni kuno timakwera lole ndipo timalipira K900 koma mafuta atangokweramu akweza kufika pa K1 200 ena K1 300.

“Kuno anthu amalima mpunga ndipo amapita nawo ku Limbe, thumba la makilogalamu 50 amatilipitsa K300 koma pano tikulipira K500,” adatero Banda, yemwe adatinso boma lichitepo kanthu.

Abdul Sapala, yemwe amameta ku Mbayani mumzinda wa Blantyre wati iye pamwezi amapeza K11 000.

Nyumba yomwe akumeteramo akuti amalipira K5 000, nyumba yomwe amakhalanso amalipira K6 000.

“Apa ndiye kuti ndalama yanga yatha komanso ndikuyenera kusamala banja. Enanso kumudzi akuyang’ana ine. Pobwera kuntchito ndimalipira K150. Ndalama yomwe ndimapeza siikuphula kanthu,” adatero Sapala yemwe amatchajanso mafoni molipitsa.

“Chipinda chometerachi akuti akukweza mtengo chifukwa cha magetsi, nyumbanso akweza, komanso minibasi akweza zomwe zikuvuta kuti tsono titani?

“Ndalama yomwe ndimagwiritsira ntchito ndiyomwe ndimapeza ndikatchaja mafoni yomwe siimakwananso K5000 pamwezi,” adawonjezera Sapala.

Iye adati ngakhale atakweza mtengo wometera kuchoka pa K100 anthu sangabwerenso ndipo wati boma lichitepo kanthu.

Amadu Kawonga yemwe amagulitsa makala kwa Chemusa mumzindawu wati kukwera mtengo kwa magetsi ndi mafuta agalimoto kukutanthauza mavuto kwa anthu.

“Kajumbo kakang’ono ka makala timagulitsa K40, koma ndikakweza mtengo anthu sangamagule. Phindu sindikulipeza chifukwa komwe timakapikula makalawa nakonso akweza mtengo.

“Ndalama zomwe ndikupeza pamwezi siimakwana K10 000 koma ndikuyenera ndisamale banja, kumudzinso akudikira ine, pamwezi ndilipire nyumba, madzi magetsi omwe akweranso mtengo. Boma lidakatsitsako mtengo wa magetsi ndi mafuta agalimoto kuti zinthu zikhale zotchipa kwa ife,” adatero mkuluyu.

Mkulu wa bungwe loona ufulu wa ogula la Consumers Association of Malawi (Cama), John Kapito wati ndi zomvetsa chisoni kuti zinthu zikumka ziyipirayipirabe.

Iye wati izi zikuchitika chifukwa boma lataya anthu ake pomwe akumva ululu kaamba ka kukwera mtengo kwa zinthu.

Kapito watinso anthu akuyenera adziwe ufulu wawo kuti atha kuchita ziwonetsero zosonyeza kukhumudwa ndi kusayenda bwino kwa zinthu.

“Tikhala tikufotokozera anthu kuti atha kuchita ziwonetsero zokhumudwa ndi kukwera mtengo kwa zinthu,” adatero Kapito.

Nduna yofalitsa nkhani, Moses Kunkuyu, wati nzoona kuti zinthu m’madera ena zaipa koma anthu asade nkhawa chifukwa chuma chikangoyamba kuyenda bwino mavuto onse atha.

“Pa miyezi 18 yomwe tidanena pali chiyembekezo kuti zinthu ziyamba kuyenda bwino,” adatero Kunkuyu, yemwenso ndi mneneri wa boma.

Related Articles

Back to top button