Chichewa

Kasambara: Akhazikitsa chimbale mwezi uno

Martha Kasambala ndi woimba nyimbo zauzimu ndipo amakhala ku Mzuzu. Iye ali ndi zimbale

ziwiri ndipo mu December muno akuti akhazikitsa chimbale chake chatsopano chotchedwa Amasamala. Mtolankhani wathu DAILES BANDA adacheza naye motere:

Ali ndi uthenga wapadera m’chimbale chatsopano: Kasambara
Ali ndi uthenga wapadera m’chimbale chatsopano: Kasambara

Tikudziweni…

Ndine Martha Kasambara wa m’mudzi mwa Malanda ku Chintheche m’boma la Nkhata Bay. Ndili pabanja ndipo ndili ndi mwana mmodzi.

 

Mbiri yako pamaphunziro njotani?

Ndidaphunzira pulaimale yanga pa Lilongwe LEA pomwe ndidalemba mayeso anga a Standade 8; sekondale ndidaphunzira ku Chipasula ku Lilongwe komweko. Ndidakapanga maphunziro a zauphunzitsi ku Tanzania komwe ndidaphunzitsa mwakanthawi pang’ono ndipo pakadalipano ndikupanga bizinesi.

 

Ndiye zoimbaimbazi mudayamba bwanji?

Ndidayamba kuimba ndili wachichepere kwambiri koma chimbale changa choyamba ndidatulutsa muchaka cha 2008 chomwe chimatchedwa kuti Zonse ndi Yesu. Chimbale chachiwiri Nganganga ndi Yesu chidatuluka mu 2010. Chimbale chatsopano chotchedwa Amasamala ndichikhazikitsa mu December muno.

 

Uthenga waukulu womwe wanyamula ndi wotani m’chimbalechi?

Kwakukulu uthenga omwe uli m’chimbalechi ndi wachilimbikitso kwa Akhristu anzanga munyengo zili zonse zomwe iwo akudutsamo. Yesu amasamala anthu ake ndipo tikamudalira iye sitidzakhumudwa chifukwa chisomo chake ndi chokwanira.

 

Kodi mfundo za munyimbo zimenezi mumazitenga kuti?

Nyimbo zanga kwambiri zimachokera pa maulaliki a kutchalitchi komanso ndikamawerenga Baibulo ngakhalenso nthawi zina zinthu zomwe ndikuona ndi kukumana nazo.

 

Ndi zinthu ziti zomwe mungakonde kuti zisinthe kumbali ya zoimba m’Malawi muno?

M’mastudio mwathu mukufunika zipangizo zamphamvu zojambulira nyimbo ngati mmene kulili kumaiko a anzathu, monga ku South Africa, chifukwa nyimbo zimamveka bwino kwambiri.

 

Phindu mukulipezamo mukuimbaku koma?

Mmbuyomu zinthu zimavuta koma pakalipano ndi chimbale chatsopanochi, tsogolo lopindula likuoneka.

 

Pa nthawi yomwe mukungokhala mumakonda kupanga chani?

Ndimakonda kuonerera mafilimu a ku India pakanema.n

Related Articles

Back to top button