Chichewa

Khama mu ulimi wa mtedza

Listen to this article

Kwa alimi monga  Lipherani Mkhupera wa m’boma la Zomba, amachengetera bwino mbewu ya mtedza kuti apindule nayo.  Chifukwa cha ichi, ulimi wa mtedza ndi gawo  lofunikira  kwambiri pa ulimi osiyanasiyana omwe amachita. HOLYCE KHOLOWA adacheza ndi mlimiyu motere:

Munda wa mtedza wa Mkhupera

Kodi ulimi wa mbewu ya mtedza mudayamba liti?

 Ulimiwu ndidauyamba  mu  1990 ndipo padakali pano, ndikusangalala kuti ndakwanitsa zaka zopyola 25 ndikulima mbewuyi.

Nanga chidakukopani pa ulimiwu n’chiyani?

 Bambo anga ankalima kwambiri mbewuyi choncho nditaona momwe amachitira komanso kupindulira, ndidaganiza zoti ndilowe m’malo mwawo.

Kodi ndi phindu lanji lomwe mungaloze kuchokera ku mbewuyi?

 Ndimapeza ndalama zomwe zimandithandiza ku ulimi osiyanasiyana umene ndimachita pa famu yanga. Mwachitsanzo, pafupifupi ndalama yonse yolipira anthu ogwira ntchito pa famuyi imachokera mu mtedza. Kuonjezera apo, phwemphwa za mtedza ndikasankhamo wabwino ndimasakaniza ku zakudya za nkhumba ndipo makoko ake ndimadyetsera akalulu.

Nanga msika wa mbewuyi mumaupeza bwanji?

Mzaka zonsezi ndakhala ndikulima mbewuyi mogwirizana ndi makampani osiyanasiyana omwe amaigwiritsa ntchito. Kuonjezera apo, ndimagulitsa mbewu ya mtedza yovomerezeka ku bungwe la Eye of the Child Malawi (ECM). Mtedza wina ndimagulitsa  kwa anthu ama bizinesi ang’onoang’ono monga ma venda pamene wina ndimaupanga nsinjiro ndikumagulitsa.

Kodi mtedzawu mumawulima komanso kuwusamalira motani?

Ulimi wa mtenda ndi umodzi mwa ulimi omwe ndiosalowa mthumba kweni kweni kusiyanisa ndi mbewu zina chifukwa sugwiritsa ntchito feteleza. Chachikulu chomwe chimafunika ndi kutsata ndondomeko zonse zoyenera.

Mwachitsanzo, timadzala mtedza mvula yoyambilira.

Pakadali pano, alimi akulimbikisidwa kubzala mtedza kutsata m’mikwasa iwiri pa mzere umodzi kuti zokolola zichuluke.

Timakonza mizele yotalikana mosachepera masentimita 75 ndipo pamwamba pake timapaphwaphatitsa. Izi zimathandiza kuti tikhale ndi mpata okwanira kuika mizele iwiri ija. Mbewu ya mtedza ndi ya Chitedze Groundnut 7 (CG7) chifukwa imacha msanga komanso imabeleka mochuluka.

Ndimabzala mtedzawu mu mapando otalikirana masentimita 15 komanso m’mikwasa yotalikiranai masentimita 30.

Ukamera mtedzawu, timalowa gawo lopalira. Mbewuyi siyenera kukhala mutchire choncho sitidikila kuti udzu ukule.

Mtedza ukakula ndipo ukayamba kutulusa dzala zomwe zimayenera kulowa m’dothi n’kuika mtedza, timayamba kubandira kapena kuti kukwezera mizere ndi cholinga choti ubereke mochuluka.

Nanga mumadziwira chiyani kuti mtedza wakhwima?

Mtedza ukakhwima, masamba ake amayamba kupanga timadontho takuda komanso amaoneka mwachikasu, ndipo  ena amathothoka. Zizindikirozi zikaoneka, ndimadziwa  kuti mtedza wakhwima choncho ndimayamba kukumba.

Ndikamaliza kukumba, ndimauyanika pa dzuwa kuti uwume chifukwa ngati sudaume bwino, umachita chuku.

Ukauma, ndimauthothola, kupeta komanso kusankha mphwemphwa kuti ukhale wabwino. Tikatelo, timaika m’matumba n’kusokera ndi kuika muchipinda chotetezeka chopita mphepo.

Muli ndi malangizo kwa ena amene akufuna kuyamba kulima mtedza ngati bizinesi?

Kwa amene ali ndi chidwi ndi ulimi wa mtedza, ndikungowalimbikisa kuti asafooke. Chofunika kuchita mu ulimiwu ndi kutsata ndondomeko zonse.

Ulimi wa mtedza tisangouyang’ana kumbali ya businesi yokha, koma tiutengenso ngati chakudya chimodzi chomwe chikhoza kutibweretsera thanzi pakhomo pathu. n

Related Articles

Back to top button