‘Kodi malubino tilowere kuti?’

Kodi tilowere kuti? M’ndani amene adzatiteteze ngati boma likulephera kubweretsa yankho?”

Awa ndi mafunso amene Ian Simbota alinawo. Simbota ndi munthu wa chialubino. Iye ndi mtolankhani ku wailesi ya MBC.

Ulendo wotsiriza wa Phiri

Mafunso a Simbota akudza kutsatira kuphedwa kwa Yasin Kwenda Phiri, 54, wa m’boma la Nkhata Bay. Phiri adaphedwa Lolemba m’sabatayi ndipo adamuchotsa manja.

Imfa ya Phiri, ndiye kuti nkhani zokhudza malubino yafika pa 162 kuchokera mu 2014.

Anthu 23 adaphedwa ndipo 10 adasowetsedwa. Komatu kuyambira 2014, palibe munthu amene walandira chilango chifukwa chokhudzidwa ndi nkhani zokhudza malubino.

Kodi vuto n’chiyani? Simbota akudabwa: “Kukhotiko kwapita nkhani zokhudza [United Transformation Movement] UTM, mpaka milandu yawo yatha ife milandu yathu ikukakamirabe kukhotiko. Vuto n’chiyani?”

“Kodi akufuna tikakhale kuti? Tilowere kuti? Poyamba amati vuto ndi ndalama, nanga ndalama za ntchito zina zikupeza bwanji? Kukhoti kudapita milandu 44 koma palibe umene udatha. Pena amati vuto ndi akafukufuku palibe, kodi titani?”

Boma la DPP lidalowa mu 2014 ndipo icho ndi chaka chimene nkhanizi zidayamba mpaka lero pamene tikupita kuchisankho yankho silidabwere.

“Zaka zisanu ndi zambiri, bwezi boma litapeza yankho pa nkhani yokhudza kuphedwa kwa alubino,” adatero Simbota.

Koma mkulu wa apolisi m’dziko muno Rodney Jose adati polisi yakhazikitsa kafukufuku kuti anjate amene adapha Phiri.

Mabungwe kuphatikizanso chipani cha UTM alankhulapo pakuphedwa kwa Phiri ndipo adzudzula khalidwelo.

UTM idati kuphedwa kwa Phiri ndi chisonyezo cha kulephera kwa boma la DPP poteteza anthu achialubino.

“Kuphedwa kwa anthu achialubino kwanyanya ndipo zikuoneka kuti boma lalephera kuthana ndi nkhanizi, ifeyo a UTM tidzaonetsetsa kuti tathana nazo,” idatero kalata yosayinidwa ndi mneneri wachipanicho Joseph Chidanti Malunga.

Mabungwe amene adzudzulapo pakuphedwa kwa Phiri ndi monga Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR), Centre for the Development of People (Cedep), Human Rights Defenders Coalition (HRDC) ndi Association of Persons with Albinism in Malawi (Apam).

Mtsogoleri wa Apam, Overstone Kondowe adati kuphedwa kwa Phiri ndi chitsimikizo kuti boma la DPP lalephera.

“Taonapo maiko amene tayandikana nawo adathana nazo kale, koma ifeyo tikulepherabe,” adatero Kondowe.

Share This Post