Koma malonjezo enawa!

Kaya zidali zoona, kaya zabodza, zimamveka kuti nthawi imene Bakili Muluzi ankafuna mpando wa upulezidenti adalonjeza zinthu zingapo. Iye adalonjeza kuti aliyense adzakhala ndi nsapato. Onenawo n’kumatinso Muluziyo adalonjeza kuti adzapereka fetereza wa ulele.

Komatu atatenga mpando, Muluzi, Atcheya, adanenetsa kuti sadalonjeze nsapato. “Nanga ndingadziwe kuti munthu wa ku Chitipa amavala sayizi yanji?” adazizwa.

Ndipo pa nkhani ya feteleza, iye adati: “Sindinati ndidzabweretsa fetereza wa ulele ayi. Ndidati fetereza wa uleya.”

Izitu ndakumbukira chifukwa cha zimene andale agundika kulonjeza pano. Zimandichititsa chidwi zimene andale amalankhula akafuna mpando.

Ndikumbuka bwino lomwe Joyce Banda nthawi yomwe amafuna kuti amusankhe pachisankho cha 2014. Amati akafika ku Nkhata Bay, amanena kuti ine kwathu ndi kuno. Akafika ku Zomba, chimodzimodzi. Kulikonse kumene iye wafika amati ndi kwawo.

Si kuti zayamba lero. Ngakhale Dr Hastings Kamuzu Banda ankanena kuti akufuna anthu ake azigona nyumba zosathonya kukamagwa mvula, azivala bwino komanso asamagone ndi njala. M’mawwu ake, iye amanena kuti dzikoli walifikitsa patali zedi, pomwe palibenso angalifikitse.

Pofuna utsogoleri, andale amalonjeza zambiri. Mawu a Richard Nixon, mtsogoleri wa dziko la America pa 20 July 1969 amapherezera izi. Iye adati atsogoleri ambiri amalonjeza anthu kuti adzawapatsa mwezi, koma osawapatsa. Iye adati ndi iye yekha amene adapereka mwezi umene adalonjeza. Izi adanena Neil Armstrong komanso Edward Aldrin atakhala anthu oyamba padziko la pansi kuyenda ku mwezi. Izi zidadza chifukwa Nixon adaika ndalama zochuluka ku kafukufuku wa za mlengalenga.

Komatu tonse tikudziwa bwino kuti Nixon adatula pansi udindo mu 1972 kaamba ka nkhani ya Watergate, inde komwe tidabera dzina la Cashgate.

Tsono n’chifukwa chiyani ndikunena zonsezi?

Ndakhala ndikutsatira bwino zimene amalankhula Saulos Chilima pa misonkhano yokopa anthu kuti adzamuvotere. Kungobenthula chabe, poyamba adanena kuti chipani chake cha UTM chidzalipirira aliyense amene adzaimire chipanicho ukhansala komanso uphungu. Lonjezo ilo.

Iye akutinso adzabweretsa sitima yothamanga zedi, yoyendera magetsi! Pamene njanji zathu zidamera mitengo, tizingodikira.

Zimandipatsa chidwi kuti amalankhula zogwirizana ndi dera limene ali. Malonjezo amakhala ochuluka. Ku Nkhotakota adalokambapo zolimbikitsa ulimi wa chamba osati chosuta. Ku Mwanza adalonjeza kulimbikitsa ulimi wa zipatso mpaka mafakitale.

Malonjezo awa, si bwino kudzatitsamwa.

Izi zili apo, palinso atsogoleri ena amene amafuna kutionetsa kuti adabadwa nawo utsogoleri. Mwachitsanzo, Peter Mutharika masiku apitawa adati iye adali mlangizi wa Masauko Chipembere ali ndi zaka 15! Chodabwitsaa n’choti nkhani yonse ya Chipembere palibe pamene pamatchulidwa dzina la Mutharika!

Naye Lazarus Chakwera amanenetsa kuti adzapitiriza pamene Kamuzu adalekezera. Malonjezo okhaokha. Ena n’kumadabwa kuti adzapitiriza zonse: Zabwino ndi zoipa pandale?

Share This Post