Woimba Joseph Nkasa m’nyimbo yake ina, amaneneratu kuti aliyense ayenera kugwira ntchito ina iliyonse kupatulapo kuba. Ngakhale
sunganeneretu kuti kuba ndi ntchito, kupewa tchimoli kuli ndi njira zambiri. Apa tikuona mnyamata wina kumsika wa Limbe kugulitsa zinkhupule poopa kuba. Ntchito nzosiyana, koma tisaiwale ndalama ndi imodzi.