Nkhani

Kukweza mafumu kwalowa ndale—mafumu

Listen to this article

Mkwezakweza wa mafumu womwe mtsogoleri wa dziko lino, Joyce Banda, wachita chitengereni mpandowu wanyanyula mafumu. Iwo apempha kuti mtsogoleriyu aziona zingapo asanakweza mafumu.

Mafumuwa, omwe sadafune kutchulidwa maina awo komanso boma lomwe akuchokera, ati pamiyezi 7 ndi theka yomwe mtsogoleriyu wakhala akulamula, ndi zosamveka kuti angakhale atakweza kale mafumu ochuluka chotere m’mipando yawo.

Iwo, omwe akuganiza kuti kukweza kwa mafumuku kumadza pazifukwa za ndale, ati akudabwa kuti m’maboma ena mulibe ‘mfumu yandodo’ (Senior Chief) koma pokweza mafumu akumakakwezanso m’maboma omwe ma Senior Chief alipo kale.

Mwachitsanzo, m’boma la Mwanza muli ma T/A awiri ndi Sub T/A mmodzi ndipo mulibe Senior Chief, yemwenso madera ena amatchedwa kuti ‘mfumu yandodo’.

M’boma la Mwanza muli ma T/A anayi koma mulibenso mfumu yandodo.

M’maboma ena monga Kasungu mfumu zandodo zilipo zinayi, Karonga imodzi, Rumphi imodzi, Chitipa ziwiri, Nsanje ziwiri, Mzimba ziwiri ndi Ntcheu ziwirinso.

“Ifenso tikudabwa kuti kodi apulezidentiwa akuyang’ananji akamakweza mafumu? Nthawi zonse akumati akuyang’ana ntchito zawo, kodi kanthawi komweka mafumu awakwezawa awawona bwanji? Bwanji m’maboma ena akukhazikitsa atambala awiri pamene ife tilibe tambala?” idatero mfumu ina, yomwe idati zotere zichititsa kuti mafumuwa azichita zosangalatsa Pulezidenti n’cholinga choti akwezedwe.

“Ntchito yathu tikugwira mokayika komanso tikufooka chifukwa sitikudziwa kuti amene awakwezawo akumawayang’ananji,” idatero mfumuyo.

Koma nduna ya maboma aang’ono, Grace Zinenani Maseko, yati sithirapo ndemanga pa nkhaniyi pokhapokha apeze mafumu omwe akudandaulawo.

“Ndiyankhulapo pankhaniyi ndikapeza mafumu omwe akudandaulawo. Sindikutanthauza kuti sindiyankhula koma ndipeze kaye odandaulawo. Sindingakuuzeni tsiku lomwe ndipeze mafumuwa,” adatero Maseko.

Bester Mandele, bwanamkubwa wa boma la Rumphi, komwe kwakwezedwa T/A Mwankhunikira kukhala STA, wati iye ngati bwanamkubwa samatengapo gawo pakukwezedwa kwa mafumu.

“Timapereka malipoti a momwe mafumu akugwirira ntchito boma lonse koma za mfumu yomwe ikwezedwe ndiye sizitimakhudza,” adatero bwanamkubwayo.

Senior Chief Kalonga ya m’boma la Karonga yati singayankhire nkhaniyi chifukwa nayonso idakwezedwa.

T/A Chekucheku ya m’boma la Neno yati ndi bwino boma lililonse likhale ndi mfumu yandodo koma ikudabwanso kuti kumeneko kulibe mfumu yandodo.

“Ufumu wa Chekucheku uli ndi mbiri yabwino monga mmene ulili ufumu wa Kwataine. Takhala tikudikira kuti nafenso tikhale ndi mfumu yaikulu chifukwatu imatithandiza zambiri,” idatero mfumuyo.

Senior Chief Kaomba ya m’boma la Kasungu yati singaikire ndemanga pankhaniyi koma pakufunika kuti pokweza ufumu pazitsatidwa ndondomeko yake maka mbiri ya mfumuyo.

Kaomba adati ngati zimenezi sizikutsatidwa ndiye kuti kukwezaku kukuchitika mwandale.

Izi zikudza pamene bungwe loona za malamulo la Malawi Law Commission lili mkati kuchititsa misonkhano yokozanso malamulo okhudza mafumu.

Malamulo a dziko lino okhudza ufumu adakonzedwa pa 29 Disembala 1967. Malamulowa amapereka mphamvu kwa mtsogoleri wa dziko, malinga ndi gawo 4 (1), kuti atha kusankha Paramount Chief kapena Senior Chief.

Boma, kudzera mu unduna wa maboma aang’ono ndilo lidapereka ntchito yokonzanso malamulowa ndipo misonkhano yomva maganizo a anthu yachitika m’zigawo zonse zitatu za dziko lino.

Lachinayi pa 27 Sepitembala 2012 msonkhanowu udachitikira ku Hotel Victoria mumzinda wa Blantyre ndipo anthu osiyanasiyana, kuphatikiza mafumu a m’maboma la Zomba, Chiradzulu, Blantyre, Neno, Mwanza, Nsanje ndi maboma ena adasonkhana.

Mfundo yomwe idakula pamsonkhanowo ndi yoti malamulowa akonzedwe kuti mtsogoleri wa dziko asamakweze mfumu pongoloza koma azidutsa kwa abanja komanso bwanamkubwa wa bomalo.

Mafumuwo adati zipani zolamula ndizo zikuwononga mbiri ndi ntchito ya mafumu chifukwa powakweza sakumayang’ana mbiri ya ufumuwo komanso khalidwe la mfumuyo.

Wapampando wa bungwe lomwe likuchititsa kafukufukuyu, Anaclet Chipeta wati ntchito yomva maganizo a anthu yatha ndipo atumiza lipoti lazomwe apeza kwa nduna ya za chilungamo.

Related Articles

Back to top button