Nkhani

Kulira kwanyanya m’zipatala

Listen to this article

Kubangula ndi kulira mokweza kukumveka m’zipatala za m’dziko muno pomwe boma lachepetsa ndalama zopita kuntchito za chipatala potsatira mavuto a zachuma amene dziko lino likukumana nawo.

Mneneri wa unduna wa zaumoyo Adrian Chikumbe wavomereza za vutoli ndipo adati undunawo udalandira ndalama zochepa kuchokera ku nthambi ya za chuma.

Odwala akuona masautso m’zipatala
Odwala akuona masautso m’zipatala

“Tikuyesetsa kuti tipeze ndalama zoonjezera ndipo pakadalipano tikuyankhula ndi mabungwe omwe angatithandize,” adatero Chikumbe.

Iye adati akuyembekezera kuti ayankhidwa mwezi uno kapena miyezi iwiri ikubwerayi.

Zipatala zachepetsa ntchito zambiri makamaka mayendedwe a maambulansi komanso chakudya chikumaperekedwa kamodzi kapena kawiri patsiku m’malo mwa katatu.

Dokotala pa chipatala cha Karonga Charles Sungani adauza Tamvani kuti achepetsa chakudya cha odwala kuchokera pa kudya katatu kufikira pa kawiri patsiku.

“Ambulansi nazo mafuta zilibe ndipo pakadali pano maambulansi akumangogwiritsidwa ntchito kunyamula amayi oyembekezera omwe ali ndi mavuto,” adatero Sungani.

Iye adati pofika sabata ya mawa mafuta amene ali nawo akhala atatha.

M’maboma a Mzimba ndi Nkhata Bay odwala akumadya chakudya kamodzi patsiku ndipo ambulasi zambiri zikungokhala kaamba ka kusowa kwa mafuta kuti galimotozo ziziyenda.

Dokotala wamkulu m’boma la Nkhata Bay Albert Mkandawire adadandaula kuti ndalama yomwe adalandira ndi yochepa kwambiri kuti ithandizire zipatala zonse m’bomalo.

“Talandira K4.8 miliyoni yomwe ikuyenera kupita ku zipatala zoposa 20. Ndalama imeneyi ndi yochepa kwambiri kuti itithandize pantchito za pachipatala,” adatero Mkandawire.

Ngakhale zinthu zili choncho m’maboma ena, monga la Dedza, sadalimve kuwawa kwambiri vutoli chifukwa aphungu a Nyumba ya Malamulo awo adagwirana manja ndi kuthandizapo.

Mneneri wa chipatala cha Dedza, Arnold Mndalira, adati achipatala adawauza aphunguwo za kuchepa kwa ndalama zomwe zidabwera kuchoka kuboma.

Mndalira adati apa aphunguwo adasonkherana limodzilimodzi ndi kuonjezera ndalama pachipatalapo.

“Adapereka K2.4 miliyoni yomwe theka lidapita ku chakudya ndipo theka lina lidapita ku mafuta a galimoto,” iye adatero.

Related Articles

Back to top button
Translate »