Chichewa

Kupewa chigodola cha nkhumba ndikotheka

Listen to this article

M’mwezi wa February chaka chino mlimi wina wa nkhumba m’boma la Lilongwe, Jeofrey Kaiyatsa, adaona ngati malodza nkhumba zake zonse zitafa ndi chigodola.

Panthawiyo n’kuti ali ndi nkhumba zazikulu zosachepera 30. Funso n’kumati: kodi zidamuvuta pati?

“Ndikuganiza kuti mnyamata yemwe ndidamulemba ntchito yosamalira nkhumbazi samayenda bwino choncho adakatenga matendawa kwina n’kulowetsa m’makola.

Tetezani nkhumba zanu ku chigodola

“Ku Lilongwe kuno sindikhalitsako chifukwa ndimachitanso ulimi wa mtundu womwewu ku Blantyre kotero kumakhala kovuta kumuyang’anira mnyamatayu,” adadandaula motero mlimiyu.

Padakali pano mlimiyu ali ku Lilongwe ndipo akukonza makola n’cholinga choti ayambirenso kuweta pogwiritsa ntchito mbewu yomwe ali nayo ku Blantyre.

Ngakhale  chigodola cha nkhumba chilibe mankhwala, mphunzitsi wa za ulimi wa ziweto wa ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar), Jonathan Tanganyika, akuti matendawa ndi opeweka.

Malingana ndi Tanganyika, mlimi asunge ndi kudyetsera nkhumba zake m’khola, asalole munthu wina aliyense kupita ku khola lake, asabweretse nyama ya nkhumba ku makola, komanso asagule nkhumba kapena chakudya chake m’mudzi momwe mwagwa chigodola.

“Kuonjezera apo, mlimi sayenera kupita kukhola la mlimi mnzake kuopetsa kutengako matendawa,” iye adatero.

Tanganyika adafotokozanso kuti ngakhale mlimi atatsimikizika kuti kumalo komwe wagula nkhumba za mbewu kulibe chigodola, akuyenera kuzisunga padera kwa masabata awiri ndipo akaona kuti sizikuonetsa chizindikiro chilichonse cha matendawa akhoza kuzisakaniza ndi zakale.

Woona za ulimi wa ziweto ku Machinga Agricultural Development Division (Maadd) Edwin Nkhulungo adafotokoza kuti mlimi yemwe nkhumba zake zidatha ndi chigodola ndipo akufuna kuyambiranso amayenera akhale osamala chifukwa kupanda kutero, vutoli lizingopitirirabe.

Iye adati mlimi ayenera kukonza bwino makola asadaikemo nkhumba zina kuopetsa nkhupakupa zomwe zimafalitsanso matendawa.

“Mlimi achotse ndowe zonse ndipo ngati n’kotheka asuke zodyera ndi zomwera nkhumba,” Nkhulungo adatero.

Mkuluyu adafotokoza kuti ngati mlimi ali ndikuthekera akhoza kutentha makola akalewo ndikukamanga ena atsopano kutali kuti asakhale pachiopsezo cha matendawa.

Tanganyika adaonjeza kuti m’khola mukalowa chigodola, mlimi ayenera kupha nkhumba zonse zodwala ndikukwirira msanga.

Iye adati malo wopherawo akuyenera kukhala wobisika, komanso wotchingidwa bwino kuti nkhumba zisafikepo.

“Tizilombo toyambitsa matendawa timakhalirira pamalo pomwe paphedwa nkhumbazo ndipo ngakhale patapita masabata angapo, nkhumba zamoyo zikafika zimatenga tizilomboti n’kuyamba kudwala,” iye adatero.

Mphunzitsiyu adafotokoza kuti nkhumba zamoyo  za m’khola limodzi ndi zodwalazo zikuyenera kuphedwa ndipo nyama yake anthu akhoza kudya kapena kugulitsa.

Malingana ndi Tanganyika, chigodola n’choopsa kwambiri chifukwa chimapha nkhumba zambiri m’kanthawi kochepa.

Mlili wa matendawa umagwa m’chaka chilichonse choncho umaopseza ulimi wa nkhumba.

Matendawa amafala kuzera mu nyama, mafupa ndi ubweya ya nkhumba yodwala ndipo chilichonse chokhudzidwa ndi zinthuzi chimanka nichifalitsa matendawa.

Kuonjezera apo, nkhupakupa zopezeka m’khola la nkhumba ndi nguluwe zimafalitsa matendawa.

Iye adaonjeza kuti zina mwa zizindikiro za matendawa ndikunyentchera, kufooka, kupeperuka poyenda,komanso kulengeza magazi pa khungu.

Tanganyika adati nkhumba zimafa zikangodwala kanthawi kochepa ndipo zina zimangofa mwadzidzidzi osaonetsa zizindikiro.

Potsiriza, katswiriyu adati mlimi ayenera kuthamangira kwa alangizi a ziweto a m’dera lake akaona zoterezi.

Related Articles

Back to top button