Chichewa

Kupewa kutsegula m’mimba

Listen to this article

 

 

 

Nthenda ya kutsegula m’mimba ndi imodzi mwa matenda omwe amakonda kufala kwambiri m’nyengo ino ya mvula.

Malinga ndi dokotala wa pachipatala cha St Lukes m’boma la zomba Siwale Shaime, kutsegula m’mimba ndi pamene munthu akuchita chimbudzi cha madzi mopitirira kanayi pa tsiku. Iye adati, nthawi zambiri chomwe chimayambitsa matendawa ndi tizilombo ting’onoting’ono tosaoneka ndi maso tomwe pa Chingerezi amatitchula kuti germs.

Zithaphwi zimasunga majelemusi otsegula m’mimba

“Nyengo ino ya mvula, matendawa amachuluka chifukwa tizilomboti timakonda kupezeka pamalo a chinyontho ndipo timafala mosavuta ndi madzi komanso ntchetche,” adatero dotoloyo.

Shaime adati mvula ikagwa, madzi othamanga amakokolola tizilomboti pamalo onyasa ndi kukatisiya m’misinje, m’zitsime ndi malo ena okhala madzi.

“Munthu akamwa kapena kugwiritsa ntchito madzi oterewa, tizilomboti timalowa m’thupi mwake ndi kuyambitsa matendawa,” adatero Shaime.

Iye adaonjezanso kuti ntchentche zimachuluka kwambiri nthawi ya mvula ndipo zimakatenga tizilomboti pamalo pomwe pali nyansi ndi kukaziika pa chakudya.

“Ntchentche zikamva fungo la chinthu choola zimathamangira ndi kukatera pomwepo, pochoka zimanyamulapo tizilomboti ndi kukatiika pa chakudya ndipo wodya chakudyachi akhonza kutsegula nacho mmimba,” adatero Shaime.

Iye adati ngakhale matendawa ndi oopsa, ndiopeweka ndipo ukhondo ndiye chida cha mphamvu.

“Anthu akuyenera kusamba m’manja ndi sopo akangochoka kuchimbudzi, asanakhudze chakudya, akasintha mwana thewera, pofuna kuyamwitsa komanso kudyetsa mwana; kukhala ndi chimbudzi cha ukhondo pakhomo, kupewa kuchita chimbudzi paliponse, kusamala ndi kutaya zinyalala moyenera, kuvindikira chakudya, kutsuka zipatso asanadye, komanso kuteteza madzi akumwa pophitsa kapena kuthira mankhwala opha majeremusi, ” adatero dotoloyo.

 

Related Articles

Back to top button