Chichewa

Kuphana kwaphweka pa Wenela

Listen to this article

Tsiku limenelo diraiva wina adati ndikhale kondakitala wa ganyu paulendo wake wolowera ku Machinjiri. Nkhani zinkakamba anthu mmenemo zidali zachilendo kwa ine.

Namwino wina, amene adatsika pa Magalasi ankanena za kachilombo koopsa ka Zika kamene kakuchititsa ana ena a ku Brazil azibadwa ndi mitu yaing’ono zedi. Nthenda zachilendo zachuluka.

art

Kuchoka apo, namwinoyo ankakamba za mankhwala oopsa otchedwa polonium-210. “Ameneyotu ndi poizoni woopsa amene wapha anthu ena otchuka. Asayansi akuti poizoni woopsayu akupezekanso mufodya yemwe ena amakwemba,” adapitiriza chiphunzitso namwinoyo.

Abale anzanga, ine nkadatolapo chiyani? Kwa ine kudali kutolera ndalama ndi kutseka chitseko.

Chongoti mayi uja tsikeni, nkhani zidasintha.

“Abale, koma tikuphana udyo. Chikuchitika nchiyani? Nkhani ing’onong’ono basi wina wafapo,” adatero bambo adakhala mpando wakutsogolo.

“Ndi chiyani koma? Ku Machinjiri kwathuku, miyezi iwiri yapitayi nkhanizi ndiye zosayamba. Wantchito wapanja wina paja adapha wantchito wam’nyumba nkuthawa ndi matumba atatu a chimanga. Wabizinesi wina wapha wabizinesi mnzake ndipo wina ndi uyu adapezeka ataphedwa nkuchotsedwa maso ndi nkhope. Zoopsa,” adayankhira wina.

“Si ku Machinjiri kokha. Mwaiwala za bambo wa ku Zingwangwa woombera mkazi ndi mwana wake nkudziphayu? Nanga mwana wa ku Mulanje wapha mayi ake nkuwakwirira m’nyumba ati chifukwa amamudzudzula kuba?” mtsikana wina amene adavala yunifomu ya sukulu ya za hotela adatero.

“Nanga uyu bambo wopha mkazi wake atapeza mauthenga a foni amene amakaikira kuti mkaziyo amatumizira bwenzi lake chonsecho mauthengawo adali a mng’ono wa mkaziyo yemwe adabwereka foni. N’chiyani chatigwera?” adafunsa mkulu wake atanyamula majumbo mosaona zoti ndi pakati pa January.

“Mawu anu ali mkamwa, simunamve za mzimayi wapezeka ataphedwa m’nyumba yogona alendo ku Bangwe?” adafunsa diraiva.

Ndidaikira mang’ombe: “Nanga za mkulu wotuma zigandanga kukapha mkazi wake wakale uja bwanji?”

Abale anzanga, ndisaname, izi zikundipatsa mantha. Thupi lamera tsemwe. Moyo wa munthu uli m’manja ndithu.

“Mungayembekeze zotani m’dziko limene mukunena kuti anthu ophwanya malamulo ena asamamangidwe? Poyamba ndimayesatu akadachotsa kaye lamulolo kusiyana ndi kuti ophwanya lamulo asamamangidwe, kapena akamangidwa azitulutsidwa,” adatero mkulu wina.

“Zoona. Anthutu ogonanana ndi abale awo alipo muno. Tsono akayamba kubwera poyera kuti nawonso alipo ochepa kwambiri ndipo ndi chilengedwe chawo kutero choncho kuwamanga nkuwaphwanyira ufulu. Chipwirikiti chobwera chikhala chotani?” adafunsa mzimayi adayandikana naye.

Aliyense m’basimo adangoti duu! Diraiva adatsegula wailesi pomwe aliyense amalingalira za nkhanizo. Padali Moya Pete. Adali maganizo athu kuti Moya Pete akambapo kanthu pa zakuphana chisawawa kukuchitikaku.

Koma ayi.

“Yesu anati akakumenyani khofi mbali iyi, mupereke linali. Otsutsa ndi a mabungwe mwandimenya mbali iyi ndakupatsani tsaya linali. Tsono Yesu sadanene kuti mukandimenyanso khofi lina ndichitenji. Mwandimenya katatu tsono ndiona umo ndingachitire,” adatero.

Mkulu wina adaseka chikhakhali. “Kodi ndimayesa Yesu adati munthu akakulakwira ka 539 uyeneranso kumukhululukiranso ka 539,” adatero iye.

Gwira bango mwaiweee! Upita ndi madzi a ng’amba.n

Related Articles

Back to top button