Nkhani

Kusanthula ntchito ya fisi

Listen to this article

Miyambo ya makolo ndi yambiri ndipo ina akuti siyofunika kupitirira chifukwa ikuthandizira kufalitsa kachilombo koyambitsa matenda a Edzi. Sabata yathayi, mafumu adali ndi msonkhano mumzinda wa Lilongwe wokambirana za miyambo. Umodzi mwa miyambo yomwe ikukanidwa ndi mwambo wa fisi omwe ambiri amausokoneza ndi mwambo wa kusasafumbi. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Senior Chief Lukwa wa ku Kasungu pa zamwambowu. Adacheza motere:

Lukwa: Mafumu tikuthana ndi miyamboyi
Lukwa: Mafumu tikuthana ndi miyamboyi

Gogo tandimasuleni eti mwambo wa fisi ndi mwambo wanji?

Pamwambowu munthu amalembedwa ganyu yobereka ana m’nyumba ya munthu yemwe zikumukanika. Imakhala ganyu ngati kuti munthu wagula galimoto koma satha kuyendetsa ndiye amalemba munthu yemwe amatha kuyendetsa kuti azimuyendetsera nkumulipira.

Basi? Nanga Fisi uja amalowa m’nyumba yoti mwini wake wamwalira kapena asungwana akuchoka kutsimba ndi uti?

Choyamba ndikonze kuti amene uja si fisi. Umene uja ndi mwambo wa kuchotsafumbi. Fisi ndi pokhapokha ngati wina akulephera kubereka ana m’nyumba ndiye pofuna kuti asachite manyazi m’mudzi, amalemba fisi kuti amuberekere mwana kapena ana koma zimakhala zachinsinsi zongodziwa bambo, mayi ndi fisiyo basi.

Nanga kusasafumbi nkutani? Ndikufunatu ndimvetsetse. Kusasafumbi kuli pangapo. Nthawi zina mwamuna akamwalira, m’nyumbamo mumabwera mwamuna wina kudzagona ndi mai osiyidwayo akuti kugoneka mzimu wa malemuyo. Nthawi zina mkazi akachotsa pakati kapena anamwali akamachoka kutsimba, amatenga mwamuna woti agonane nawo pokhulupirira kuti kutero ndiye kuti ayendetsa mwambo momwe uyenera kukhalira.

Malipiro ake amakhala chiyani?

Zimatengera pangano la awiriwo, ena amatha kulipirana mbuzi kapena nkhuku mwinanso ndalama. Apa palibe dipo lenileni lokhazikika chifukwa nzachinsinsi moti ozidziwa amakhala okhawo okhudzidwa.

Nanga pambuyo pake fisi atatembenuka kuti akufuna ana ake zingathe bwa?

Ichi nchibwana chachikulu chifukwa potengera momwe mwambowu umayendera, iye akagwira ntchito pathupi nkuoneka, akangolandira zake basi kwatha zammbuyo muno nza eni nyumbayo. Kuchita masewera, akuluakulu akhoza kugwirapo ntchito chifukwa woteroyo waphwanya mwambo wachinsinsi omwe adavomereza yekha.

Boma ndi mabungwe amati miyambo yotereyi ndi yoipa makamaka nkubwera kwa kachilombo koyambitsa matenda a Edzi, muti bwanji?

Zimenezo nzoona zokhazokha moti mafumu kuyambira ku Chitipa mpaka ku Nsanje, Nkhotakota mpaka Mchinji tidagwirizana chimodzi kuti m’madera mwathu miyamboyi isamachitike. Tidachita izi dala

chifukwa omwe amazunzika kwambiri ndi amai ndi asungwana chifukwa kumatheka bambo mmodzi kusasafumbi asungwana kapena amai angapo choncho matenda a Edzi sangathe ayi.

Nanga poti mwambo ndi mwambo, mungathe kuwaletseratu anthu?

Mfumu siyilephera makamaka pomwe ikutsogolera anthu ake pachinthu chabwino. Monga ndanena kale, mafumu tidamanga fundo imodzi moti kumupeza wina akuchita khalidweli, timamulanga potengera malamulo omwe tidamanga komanso timaonetsetsa kuti onse okhudzidwawo akayesedwe kuchipatala ngati sadavulazane ndi matenda.

Malangizo anu ndiwotani kwa anthu omwe satha kubereka koma amafunitsitsa kukhala pa banja?

Malangizo ndi wosavuta: kuli bwino asakwatire kapena kukwatiwa apo biii, alimbe mtima kudzasekedwa osada nkhawa ayi. Chomwe ife tikunena ngati mafumu nchakuti asakwatilire dala akudziwa kuti zimawavuta kenako azidzalowetsa fisi m’nyumba. n

Related Articles

Back to top button