Nkhani

Kusowa kwa magazi, mankhwala ku Qech

Listen to this article
Odwala kuchipatala cha Queens amakumana ndi zokhoma
Odwala kuchipatala cha Queens amakumana ndi zokhoma

Mavuto akhodzokera pachipatala cha Queen Elizabeth Central Hospital (QECH) mumzinda wa Blantyre. Kusowa kwa magazi ndi zipangizo kukuika miyoyo ya odwala pachiswe chifukwa chosowa chithandizo.

Lolemba ndi Lachiwiri pamene Tamvani idaswera pachipatalapa m’sabatayi idadzionera zokhoma. Imfa za anthu si nkhani yachilendo, pamene odwala ena angogonekedwa kudikirira tsiku lodzapezeka mankhwala.

Dotolo wina amene tidamupeza m’chipatalachi adati vuto lakula pachipatalapa ndi kusowa kwa magazi komanso mankhwala.

“Mankhwalawa ndiye sadayambe pano kusowa koma magaziwa ndiye avutitsitsa, mwina nchifukwa choti ana atsekera sukulu.

“Mankhwala alipo ochepa kuyerekeza anthu amene chipatalachi chimalandira,” adatero dotoloyu.

Mlembi muunduna wa zaumoyo Chris Kang’ombe akuti vutoli lilipo ndipo lipitirira ngati sipakhala kusintha pa ndalama zomwe undunawu umalandira.

“M’ndondomeko yachuma ya 2013/2014 timafunikira K28 biliyoni koma tidalandira K6 biliyoni. Timafuna mankhwala amitundu yoposa 1 000 ndiye kugula mankhwalawa kumadya ndalama zambiri. Tangoganizani tikufunikira $115 miliyoni (pafupifupi K553 biliyoni) yogulira ma ARV okha ndiye ndalama yomwe timalandira sikukwana,” adatero Kang’ombe.

Iye adati m’ndondomeko ya zachuma ya 2014/15 akufuna K32 biliyoni yogulira mankhwala koma adakaika ngati ndalamayi iperekedwe yonse.

Naye mneneri wabungwe lotolera magazi la Malawi Blood Transfusion Service (MBTS) Allen Kaombe adati mavuto osowa magazi akhudza zipatala zonse m’dziko muno.

Iye adati kusapereka magazi mokwanira ndiko kwachititsa kuti mavutowa akhudze zipatala m’dziko muno.

“Tikulephera kutolera magazi amene timawafuna omwe ndi mauniti 80 000 pachaka, mmalo mwake tikutolera mayuniti 50 000. Tikawerengetsa bwino, timayenera kutolera mayuniti 7 000 pamwezi ndi 320 patsiku. Izi sizikuchitika, tikungotolera 4 200 pamwezi ndi 190 patsiku,” adatero Kaombe.

Kaamba ka mavutowa, sizikudabwitsa kumva anthu akumwalira komanso ena kusowekera pogwira mzipatala maka cha QECH chomwe tidayenderako.

Samalani ndi woyang’anira odwala amene tidamupeza muwodi ya 4A. Iye amasamalira akazi ake amene amachokera m’mudzi mwa Elema kwa Senior Chief Nthache m’boma la Mwanza.

Iye akuti adafika pachipatalapa Lachiwiri pa 29 July mkaziyo atadwalika chifuwa chachikulu komanso kusowa kwa magazi.

“Timafika pano cha m’ma 2 koloko usiku. Ku Mwanza timanyamuka cha m’ma 12 koloko matenda atakula. Chipatala cha Mwanza ndicho chatitumiza kuno chifukwa kumeneko mankhwala komanso magazi palibe,” adatero mkuluyu.

Pa 29 atafika, Samalani adauzidwa kuti magazi palibe.

Iye adati: “Tidasowa kopita, adatigoneka kuti tidikirire mpaka atapezeka. Pa 30, botolo limodzi lidapezeka. Litatha, adati ena sapezekanso. Takhala tikudikira ndipo ena apezeka lero [pa 5 August] koma akuti akatha ndiye angotitulutsa chifukwa kulibiretu.”

Samalani akuti sipakudutsa tsiku maliro osachitika muwodi yawo zomwe zikumupatsa mantha.

“Ku Mwanza tabwerako anthu awiri, anzathuwo amwalira, moti patsiku anthu awiri kapena atatu akumwalira,” adatero iye.

Ngati sipakhala kusintha pa ndalama zopita ku undunawu ndiye anthu ngati Samalani akhala pavuto losasimbika.

“Nchifukwa chake tikumema anthu kuti apite akapereke magazi kuti anthu otere athandizidwe,” adatero Kang’ombe amene akuti mavuto a kusowa kwa mankhwala kwasintha poyerekeza ndi mwezi wa December wapitawo.

Naye Kaombe sakudziwa tsiku lomwe magazi ayambe kupezeka m’zipatalazi. “Kukhala kovuta kuti tipeze magazi chifukwa tikulephera kupeza mlingo omwe timafuna pamwezi. Mavutowa angathe tsiku lililonse ngati dziko titagwirana manja kuti tipereke magazi mwaunyinji.”

Kaombe adati mavutowa akula kwambiri chifukwa ophunzira amene amapereka magazi kwambiri atsekera.

“Malita 85 mwa 100 a magazi amene timatolera amachokera kwa achichepere omwe ndi azaka pakati pa 16 mpaka 25 pamene nambala yotsalayo imachokera kwa akuluakulu azaka 26 mpaka 65. Pamene sukulu zatsekera, tikuvutika kuti titolere magazi,” adatero Kaombe.

Related Articles

Back to top button