Chichewa

Kutambasula unamwali wa mtete

 

Nyazgambo kuonetsa momwe ankavinira

Ndakupezani kuno ku Embangweni. Tatiuzeni zambiri za mtete.

Mtete ndi unamwali womwe kalelo ankatilangira. Ankatitsekera m’kachipinda komata kwa sabata imodzi kwinaku akutiphunzitsa zambiri zoyenera kuchita tikadzakwatiwa.

Talongosolani bwinotu pamenepo?

Mwa zina ankatiphunzitsa magwiridwe a ntchito tikamacheza ndi abambo. Apatu nkuti tikuimbira kanyimbo: Ko! Kokoliko! Ko! Kokoliko! Tambala walira ayiye timpatse malango!

Nyimbo imeneyi timavina titamangira nsalu m’chiunomu. Nsaluyi imathandizira guleyu.

N’chifukwa chani adakuphunzitsani kuvina mtete?

Nyazgambo kuonetsa momwe ankavinira
Nyazgambo kuonetsa momwe ankavinira

Ine adandiuza kuti ndizivina mtete chifukwa ndikapita ku banja opanda mtete, mwamuna akandisiya. Ndiye iii! tinkamvera ndi chidwi kwambiri kuti potha pa sabatayi tikhale titadziwa kuvinako komanso titamva mwambo wonse omwe agogo adali kutilangiza. Agogowa ankatiphunzitsa kuvinaku tsiku lililonse.

Tidakhala sabata yatunthu tili m’nyumba pamenepo anzathu adali kusukulu.

Ankati mwamuna akakusiyani chifukwa chiyani?

Akuluakulu ankati popanda mtete, basi mwamuna akapeza wina ndipo ankatiphunzitsiratu zoyenera kuchita.

Palinso china chomwe mudaphunzira?

Eya, ankawalanganso atsikana amwano ku unamwali omwewu. Amawaveka chitenje atachimanga ngati kabudula, akuvina namazungulira ndi matakowa. Kwinaku akutchula za mwano zonse zomwe amawachitira makolo awo.

Kodi unamwaliwu udathandizirapo kuti mudye mfulumira, ndi cholinga chokachita zomwe mudaphunzirazo?

Kumbali yanga ayi ndithu, chifukwa alangizi ankaneneratu kuti tidzisunge mpaka tsiku lodzalowa m’banja. Komabe ndikudziwa atsikana anzanga omwe adatenga mimba chifukwa chofuna kuyeserera zomwe tidaphunzira zija.

Nde mwati amalanganso atsikana amwano komweko?

Nthawi zina makolo amatumiza ana awo ku unamwaliwu akakhala nkhutukumve. Awa amakhala atsikana wosatumikira makolo. Uku ndiye kumakhala kulangidwa, mbali inayi monga ndanena kale akuvina mokhwekhwereza matakowa. Apatu ndiye kuti agogo akulandizana nyimbo kwinaku akuwaitana maina awo, nkumatchula za mwano zomwe amawachitira makolo awo.

Mwachitsanzo chabe ankati: Jane katunge madzi ku dambo ndipo woyankhira ankati ayi sindikufuna.

Kodi izi zimathandiza kuthetsa mwanowo?

Zimathandiza chifukwa amatuluka osinthika ndithu. Mwano uja umathera komweko.

Kodi padali zomuyenereza mtsikana kulowa ku unamwali umenewu?

Unamwaliwu amalowa ndi mtsikana wotha msinkhu. Sikumalowa ana. Koma zaka 12 kupita mtsogolo ndipo akhale woti wagwa m’dothi.

Nanga tsiku lotuluka likakwana, ndi malangizo anji omwe mudali kulandira?

Akuluakulu adali kutilangiza kuti tisakasiye kuvina mtete kuti tikazolowere (Mtete uwu mungalekenge cha kuvina).

Kodi zidakuthandizani?

Pamenepa ndingangoti, ndimadziwa ndithu.

Kodi unamwaliwu ukadalipo?

Ayi ndithu. unamwaliwu udatha kaamba kakubwera kwa amabungwe ophunzitsa

za maufulu osiyanasiyana komanso olimbikitsa kuti atsikana asamathamangire kukwatiwa koma azilimbikira sukulu. Adatiuza kuti kudali kolakwika kuchita izi chifukwa anawa adali kujomba  kusukulu kwa sabata yatunthu zomwe zimasokoneza maphunziro awo. Komanso adati ndi zina mwa zomwe zimalimbikitsa ana akazi kulekeza sukulu panjira ndi kukwatiwa msanga.

Kodi pakadalipano, poti mwakula, mungavomereze mwana wanu apite ku unamwaliwu?

Ayi ndithu. Ine mwana wanga yemwe ali ndi zaka 10 tsopano sindingafune kuti adutse zimenezi. Inde, ine ndidapitako koma mwana wanga yekha akadzatha msinkhu, ndidzamulangiza ndekha ndikuyitana anzanga ena basi. n

Related Articles

One Comment

  1. Pathetic!! It reminds me of a story on BBC right now concerning an HIV positive “hyena” man in Nsanje. We Malawians are losers. And we have exactly a country and leadership we deserve. Mxii!!!

Back to top button