Chichewa

Likodzo limatha magazi m’thupi

Listen to this article

Likodzo ndi matenda amodzi amene akapanda kuzindikiridwa msanga akhoza kupha munthu chifukwa amayamwa magazi.

Michael Luhanga amene ndi katswiri pa matenda a likodzo kuofesi ya zaumoyo ku Zomba adati likodzo limafala ngati munthu amene ali ndi likodzolo wakodzera m’madzi ndipo nkhono zimene zimanyamula tizilombo ta nthendayi tikhudzanso munthu wina amene alibe likodzo.

“Ndi bwino kupewa kukodzera m’madzi kapena kuchita chimbudzi patchire chifukwa madzi a mvula akakokolola zimenezi ndi kukathira mumtsinje ndiye kuti anthu onse amene akugwiritsa ntchito madziwo ali pachiopsezo chotenga likodzo,” adatero Luhanga.

Luhanga: Nthawi ya mvula ndi yofunika kusamala

Malinga ndi Luhanga likodzo lilipo la mitundu iwiri: la m’matumbo komanso la m’chikhodzodzo.

“Zizindikiro zooneka ndi maso kuti munthu ali ndi likodzi ndi kukodza timadontho ta magazi makamaka akamamaliza kukodza,” adatero Luhanga.

Kupatula kutha magazi m’thupi, likodzo limachititsanso kuti ana azikula monyentchera, ana amakula opanda nzeru, kusabereka kwa amayi, khansa ya khomo la chiberekero, kutupa kwa kapamba ndi chiwindi komanso kudzadza kwa madzi m’mimba.

“Ndi  bwino kuti anthu akaona kuti akukodza magazi azithamangira kwa alangizi a zaumoyo kudera lawo kapena kuchipatala matendawo asanayale maziko m’thupi mwawo,” adatero Luhanga.

Katswiriyu adati anthu amene ali pachiopsezo chachikulu chotenga likodzo ndi ana chifukwa amakonda kusewera m’madzi akuda a mvula komanso anthu amene amalima mpunga kumadambo ndi mbewu zina ndi amene ali pachiopsezo chotenga likodzo.

“Tikulangiza anthu kuti azigwiritsa ntchito zimbudzi akafuna kudzithandiza chifukwa kukodza kapena kuchita chimbudzi paliponse ndi koopsa masiku ano a mvula,” adalangiza Luhanga.

Iye walangizanso kuti likodzo ndi lochizika chifukwa wodwala amapatsidwa mankhwala a praziquantel  amene amathaniratu ndi likodzo m’thupi.

“Tilimbikitse anthu kuti asamachedwe ndi njira zina zochizira likodzo zimene akuzidziwa koma azithamangira kuchipatala chifukwa akabwera mochedwa njira zawozo zitakanika moyo wa odwalayo amakhala kuti auyika pa chiswe,” adatero Luhanga. n

Related Articles

Back to top button