Chichewa

Ma Queens alephera ofikafika

 

Malawi Queens meet Jamaica today
Malawi Queens meet Jamaica today

Zowawitsa! Mpake Mwawi Kumwenda ndi Sindi Simtowe adalira ching’ang’adza Lachisanu atalephera pango’nong’ono kuwolotsa ma Queens kuti afike m’ndime ya semifainolo mumpikisano wa chikho cha mpira wa ntchemberembaye cha padziko lonse (World Netball Cup), womwe ukuchitikira ku Sydney m’dziko la Australia. Iwowa adagonja ndi timu ya Sunshine Girls ya ku Jamaica ndi zigoli 63 kwa 62. Kunena zoona, ma Queens adachita ‘chamuna’ ndipo Mmalawi aliyense ayenera kunyadira kuti iwo sadachititse dziko manyazi. Aliyense, osewera ndi makochi awo adadzipereka, koma tsoka likalimba ndi mmene zimakhalira. Amati nguluwe idalira msampha utaning’a—akadangoipambana apa basi zikadetha kuti Malawi ikhale mu Top 4 padziko lapansi. —Joseph-Claude Simwaka

Related Articles

One Comment

Back to top button