Mafizo amathandiza anthu achikulire

Woona za mafizo pa chipatala cha anthu achikulire cha Kalibu ku Lilangwe m’boma la Blantyre Veronica Mughogho akuti mafizo ndiothandza kwambiri pa miyoyo ya anthu osachepera zaka 60.

Mughogho adati mafizo amathandiza anthu a misinkhuyi kuti asakalambe msanga komanso  kupewa mavuto ndi matenda osiyanasiyana omwe amadza kaamba ka ukalamba.

Mughogho: Thandizoli ndi laulere

“Mafupa komanso mokumanira mwake mumalimba bwino choncho munthu savutika ndi kupweteka kwa miyendo, msana ndi ziwalo zina,” iye adatero.

Dotoloyu adati  ichi n’chifukwa chake kwa nthawi yoyamba m’dziko muno mwakhazikitsidwa chipatalachi ndi cholinga choti ukalamba usakhale chipsinjo.

Mughogho adafotokoza kuti thandizo ku chipatalachi ndilaulere choncho munthu wina aliyense yemwe wafika zakazi kupita m’mwamba apite akathandizidwe.

Iye adati chipatalachi sichamafizo okha koma chikupereka thandizo la matenda osiyanasiyana malingana ndi vuto lomwe munthu wabwera nalo.

“Timalimbikitsanso anthu omwe ataya mtima chifukwa cha matenda omwe ali nawo monga a khansa ndi cholinga choti akhale ndi moyo wathanzi,” adatero dotoloyu.

Mughogho adati chipatalachi chimagwira ntchito kuyambira Lolemba kulekezera Loweruka kuyambira nthawi ya7:30 m’mawa mpaka 5:00 madzulo.

Iye adati pachipatalapa pali akadaulo a matenda osiyanasiyana.

“Masomphenya athu ndi oti kutsogoloku tidzakhale ndi zipinda zoti odwala omwe akuyenera kugonekedwa azizagonera pomwepa, tizidzachita anthu maopoleshoni osiyanasiyana ndi zinthu zina zikuluzikulu zofunikira pachipatala,” adatero dotoloyu.

Mughogho adafotokoza kuti chipatalachi chikufuna anthu akufuna kwabwino athandizire ndicholinga chopititsa patsogolo miyoyo ya anthu achikulire m’dziko muno. n

Share This Post