Nkhani

Mafumu a ku Zambia akulowerera kwa Mkanda

Listen to this article

Pamene nkhani ya mpungwepungwe wa nyanja ya Malawi pakati pa dziko lino ndi la Tanzania ili mkamwamkamwa, nawo mafumu ena a dziko la Zambia ali pakalikiriki kugawira anthu awo malo mbali ya dziko lino kwa mfumu yaikulu Mkanda m’boma la Mchinji.

Malinga ndi mfumu yaikulu Mkanda, mkangano wa malo kumalire a dziko lino ndi Zambia udayamba zaka za m’ma 1970.

Mkanda adauza Tamvani m’sabatayi kuti kuchokera m’zakazi kumaloku kwakhala kukufika akuluakulu a boma ochokera ku Chipata m’dziko la Zambia, Blantyre ndi Lilongwe kukakambirana zothana ndi mpungwepungwewu.

“M’chaka cha 1998 kapena 1999 kudabwera anthu aboma kudzakambirana, koma vutoli likadalipo ndithu; akugulitsa malowa ndi Chanje komanso Mkandamateyo yemwe ndi mwana wa a agogo yemwe adatsalira ku Zambia nthawi ya chitaganya cha Rhodesia ndi Nyasaland,” idatero mfumuyi.

Iyo idati mfumu Chanje yalowerera maesiteti ochulukirapo a Mpale, Chimwamkango, Chimwemwe, Mthyolasenje ndi Chankhungu pomwe Mkandamateyu amamvetsa ndi kusiya kulowereraku akauzidwa kutero.

“Kuno milandu ya malo simatha, timangokhalira kukangana ndi anzathu a ku Zambia omwe ativutitsa kwabasi, iwowa sakulemekeza mabikoni omwe adaikidwa kumaloku,” Mkanda adatero.

Iye adati izi zakhudza anthu ake omwe akusowa malo olima.

Polankhulapo pankhaniyi, DC wa boma la Mchinji, Yamikani Chitete, adati ofesi yake yakhala ikulandira madandaulo kuchokera kwa eni maesiteti omwe alowereredwawa.

“Mwezi wa May kunabwera anthu kudzadandaulanso za nkhaniyi ndipo tinawauza kuti tifikako mavoti a patatu akadutsa, choncho ine ndi anzanga a ku Chipata tipitako Lachisanu [dzulo],” Chitete adatero.

Bwanamkubwayu adati mmbúyomu kumaloku kudapitidwanso pamodzi ndi bwanamkubwa wa boma la Chipata ndipo atawalankhula anthuwo adachoka mokakamizidwa ndi apolisi a dzikolo.

Related Articles

Back to top button