Mafumu atsegula Njira ya kampeni

Pamene kampeni yafika pachiindeinde, zipani zandale zati n’zokhutira ndi momwe mafumu akuperekera mwayi wochititsa misonkhano yokopa anthu m’madera mwawo kwa zipani zotsutsa.

Katswiri wa za ndale, George Phiri, wati zimaterezimatere bwenzi zikoma ndipo wayamikira mafumu potsegula njira kwa zipani zonse.

Tsopani MCP ikuchititsa misonkho yokopa anthu ku Thyolo momasuka

Bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) lisadatsegulire kampeni mafumu ena amaletsa zipani za Malawi Congress Party (MCP) ndi UTM kuchititsa misonkhano yokopa anthu m’madera mwawo.

Mwachitsanzo, mafumu a ku Thyolo amakaniza zipani za MCP ndi UTM kuchititsa msonkhano m’bomalo kaamba koti “ndi kuchipinda kwa mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, ndi chipani chake cha Democratic Progressive Party [DPP]”.

Mneneri wa MCP, Maurice Munthali, adati mmbuyomu chipani chake chidakonza msonkhano kwa Bvumbwe m’boma la Thyolo, koma mafumu adachiuza kuti ena apempha kale malo a msonkhanowo, zomwe adati zidali zabodza.

“Tidazindikira pammbuyo pake kuti n’zabodza popeza padalibe yemwe adapempha malowo.

“Posachedwapa tidapemphanso ndipo adatilola. Tidachititsa msonkhano opanda vuto lililonse. Izi zikusonyeza kuti zinthu zasintha,” adatero Munthali.

Naye mlembi wa UTM, Patricia Kaliati, adati mmbuyomu mafumu adawaletsa kuchititsa msonkhano wokopa anthu kwa Folopeni m’bomalo, komanso adauza anthu a m’midzi yawo kuti asapite ku msonkhanowo.

“Koma padakali pano tikapita akumatilandira n’kutilola kuchititsa misonkhano opanda vuto lililonse chifukwa cha ndondomeko zomwe MEC idakhazikitsa,” adatero Kaliati.

MEC idasayinitsa mafumu ndondomeko zoti atsatire nthawi ya kampeni. Mwa zina, mafumu sakuyenera kukondera kapena kuletsa zipani zotsutsa kuchititsa misonkhano yokopa anthu m’madera mwawo.

Mlembi wa UDF, Kandi Padambo, adati kapeni isadayambe chipani chake chikhala chikukumana ndi mikwingwirima yosiyanasiyana m’chigawo chakumpoto komwe chimakachititsa misonkhano yokopa anthu.

Iye adati UDF idatsala pang’ono kusiya kupita m’chigawocho chifukwa cha mavutowo.

“M’malo angapo tidabwedzedwa, koma osatiuza zifukwa zake.

“Koma panopa tikapita m’madera omwe aja akumatilandira n’kutipatsa mwayi wochititsa misonkhano,” adatero Padambo.

Mfumu Lukwa ya m’boma Kasungu idati ngati mafumu amachitadi zimenezo amalakwa.

Katswiri wa za ndale Phiri adati n’zokoma kumva kuti mafumu tsopano akupereka mwayi wochititsa misonkhano kwa zipani zonse.

Iye adati zomwe mafumu akuchita n’kulambula njira yoti m’dziko muno mudzachitike zisankho za mtendere. n

Share This Post