Chichewa

Manifesito ya UTM mulinji?

Listen to this article

Akadaulo pa ndale ayamikira manifesito ya chipani cha UTM kuti ikuyankha mavuto amene dziko lino likukumana nawo komabe achenjeza chipanichi kulonjeza zokhazo zomwe akuganiza kuti zidzatheka.

Chilima kupereka manifesito kwa mmodzi mwa amene adafika ku Dowa

UTM ndi chipani chachitatu kukhazikitsa manifesito yake, pomwe zipani za Umodzi Party komanso Malawi Congress Party (MCP) adatulutsa kale manifesito awo, pomwe chipani cha UDF chikuyembekezeka kutulutsa manifesito yawo pa 7 April. Chipani cha DPP chati chitulutsabe manifesito yawo.

Potsatira kukhazikitsa kwa manifesito ya UTM Party Loweruka ku Dowa, akadaulo pa zandale Ernest Thindwa wa ku Chancellor College komanso George Phiri wa ku University of Livingstonia (Unilia) adathirirapo ndemanga pa manifesitoyo.

Thindwa adati manifesito a UTM ili ndi tokoma tomwe tingasinthe dziko lino monga kuchepetsa mphamvu za mtsogoleri wa dziko, kulembedwa ntchito kwa anthu 1 miliyoni chaka chimodzi, kumasula ku nsinga za ndale nyumba youlutsa mawu ya boma ya Malawi Broadcasting Corporation (MBC), kupeza yankho lothanirana ndi kuphedwa kwa anthu achialubino komanso kubwera ndi ndondomeko zaumoyo ndi sukulu.

“Izi ndi zofunika zitachitika m’dziko muno ndipo ndi zosavuta kuchita koma vuto lilipo n’kuti anthuwa akalowa m’boma sachita, amaiwala zomwe adalonjeza,” adatero Thindwa.

Thindwa akuti ngakhale manifesito ya UTM payokha angapangitse kuti anthu awavotere ponena kuti anthu a m’dziko muno amavotera munthu poyang’ana chigawo chomwe akuchokera kuiwala mfundo zomwe wasanja.

Pamene Phiri adagwirizana ndi Thindwa kuti manifesitoyo ili bwino chifukwa yalunjika zambiri zomwe zingasinthiretu Malawi.

Phiri adasanthula mfundo ya ulimi wa mthirira, kubweretsa mafakitale okonzera mbewu zomwe zimalola bwino m’madera mwawo ponena kuti izi n’zofunika.

“Zambiri m’dziko muno timaitanitsa kunja zinthu zoti tokha tikhonza kupanga, ngati UTM ingadzakwaniritse izi chikavoteredwa ndiye kuti tidzakhala odzidalira tokha,” adatero iye.

ZOMWE UTM YALONJEZA

Chipani cha UTM ngati chingavoteredwa pa 21 May pano, chati chidzathetsa ndondomeko yomwe boma limagwiritsira ntchito posankhira ophunzira m’sukulu za ukachenjede yomwe imadziwika kuti Quota System.

UTM yati idzamasula wailesi ya boma ya MBC kunsinga za ndale ndipo zipani zonse zidzidzamveka pa wailesiyo.

Pankhani ya bwalo la ndege, UTM yati idzakulitsa bwalo la Chileka ndi Kamuzu International Airport. Komanso kumanga mabwalo a ndege m’maboma a Mangochi ndi Mzuzu kuyambira m’chaka cha 2020 mpaka 2021. Chidzamanganso bwalo lina m’boma la Salima, kukonzanso bwalo lina ku Karonga. 

Kumbali ya maulendo a sitima, UTM yati idzamanga njanji yabwino yolumikiza Lilongwe ndi Blantyre. Kukozanso Nkaya, Salima ndi Mchinji. Komanso njanji yodutsa Limbe kudutsa Sandama kupita ku Makhanga ndi Marka m’boma la Nsanje.

Kumbali ya misewu, UTM yati idzayamba kukozanso misewu ikuluikulu kuti izigwirizana ndi momwe maiko ena zilili.

Chipanichi chikuti pofika m’chaka cha 2014, maboma onse adzakhala ndi misewu ya phula. Komanso misewu ya m’mizinda idzakhala yapamwamba monga zikhalira m’maiko akunja.

UTM yati idzamasula bungwe la Admarc DMARC kunsinga za ndale ndipo katangale amene wazinga bungwelo adzatheratu.

Chipanicho chatinso tidzalimbikitsa kholola wa madzi m’maboma onse cholinga nkhani ya kusowa kwa madzi idzakhale mbiri yakale, izinso zidzathandiza anthu kumalira nthawi zonse.

Kumbalinso ya ulimi, UTM yati idzalimbikitsa alimi kuti izizapanga ulimi wa m’magulu. Izi zidzathandiza kuti alimi azizalandira uphungu komanso kugulitsa zinthu zawo mosavuta.

UTM yatinso kumbali ya zipangizo zotsika mtengo, boma lawo lidzabwera ndi ndondomeko yoti alimi onse apeze zipangizo zotsika mtengo. n

Related Articles

Back to top button
Translate »