Masalamusi asokoneza maphunziro ku Lunzu

Sukulu ya sekondale ya Lunzu mu mzinda wa Blantyre idatsekedwa kwa sabata imodzi kaamba ka masalamusi omwe amachitikira atsikana pa sukulupo.

Msangulutso wauzidwa kuti atsikana kuti atsikana apasukuluyi amadzipindapinda modabwitsa ndipo akafunsidwa, amayankha kuti akumva kupweteka muti ndi m’thupi.

Padafunika kuti ophunzira a pasukuluyo ayambe akapitidwa kaye mphepo zina kwawo

 Chodabwitsa nchoti atapita nawo ku chiatala, madotolo sadawapeze ndi matenda aliwonse. Izi zidachititsa unduna wa maphunziro kutseka sukuluyo kuyambira Lachiwiri mpaka Lamulungu kuti ophunzirawo akapitidwe mphepo zina kwawo.

Pakadali pano, m’phunzitsi wamkulu pa sukuluyo Collins Champiti adati maphunziro tsopano abwelera m’chimake ndipo ophunzirawo ayambanso kulemba mayeso a teremu yachiwiri.

“Sitikudziwa kuti kwenikweni chidali chiyani chiyani chifukwa nawo ophunzirawo sakuthanso kufotokoza zimawachitikira; amangoti msana umawapweteka, achipatala ndi aja sadawapeze ndi vuto lililonse,” adafotokoza a Champiti.

Komatu napo pa sukulu ya Mpala m’boma la Mulanje, ophunzira adaphunzira ndi mantha sabata yapitayo pomwe wophunzira wa Sitandade 7, Judith Paulo, adawuza anzake kuti adakumana ndi masamusi ali pasukulupo.

Paulo adaona K500 yopinda ili pansi pafupi ndi kalasi yake, ndipo akuti ayitole, ndalama ija idasanduka K5 ya chitsulu. “Ndili kusukulu, ndidatsanzika kupita kukamwa madzi, pobwerera ndidaona K500 yopinda, ndikuti nditole ndidangoona yasanduka K5 yachitsulo. Komabe ndidaitola,” adafotokoza wophunzirayo.

Izi zidamuziziritsa thupi ndipo adaganiza zokanena kwa aphunzitsi omwe adamuwerutsa kuti akawauze makolo ake.

Koma akupita kwawo ndi mnzake yemwe adamuperekeza, zinthu zidasintha chifukwa adayamba kuona chidima m’maso komanso mayi yemwe adanyamula nsupa yofiira.

“Ndidamva kuwawa pamtimapa ndi pa liwombo ndipo ndidagwa pansi, mnzanga uja adakawauza makolo anga zomwe zidandichitikirazo,” adatero Paulo.

Wophunzirayo adatinso atafika kunyumba makolo ake adamutengera kuchipatala komwe adamupeza ndi malungo komanso kwa abusa omwe adamupempherera kuchotsa masalamusiwo.

Mayi a mtsikanayu adati mwana wawoyo akudandaula kupweteka pamtima komanso kuotcha paliwombo.

Koma mphunzitsi wamkulu pasukuluyo Jones Chilimwe adati zomwe akunena Paulo n’zopanda umboni chifukwa kafukufuku wawo akuonetsa kuti palibe adayiona ndalamayo kupatula mnzake mmodzi.

Iye adati akuganizira kuti awa sadali masalamusi koma mphamvu ya malungo aku ubongo.

“Kafukufuku wathu akuonetsa kuti iyi ndi mphamvu chabe ya malungo paja amabwera mosiyana koma si za masalamusi,” adafotokoza Chilimwe.

Iye adauza ophunzira onse pasukuluwo kuti asachite mantha.

Chilimwe adati pakadalipano zinthu zabwerera m’chimake pasukulupo.

Aka sikoyamba masalamusi kuchitika m’sukulu za m’dziko muno chifukwa masiku apitawo, nayo sukulu ya atsikana ya Karonga idatsekedwa pomwe ophunzira ena ankachitanso zachilendo. n

Share This Post