Nkhani

Masitalaka: Bwanji APM sakulankhulapo?

Zafika pa mwana wakana phala. Akuluakulu a mabungwe komanso zipani apempha mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika kuti alankhulepo pa kunyanyala ntchito kwa ogwira m’boma komwe kwafika pa lekaleka m’dziko muno.

Izi zikudza patatha mwezi mabwalo a milandu ali otseka, nazo sukulu za College of Medicine ndi Chancellor College (Chanco) zidatsekedwa kaamba ka sitalaka. Pothira mchere pabala ndiye ndi abungwe lothana ndi katangale la ACB lomwe maofesi ake atsekedwa Lachiwiri lapitali, komanso ogwira ntchito kuchipatala cha Kamuzu Central Hospital amenenso ayamba kunyanyala pofunitsitsa kuti boma liwakwezere malipiro awo.

Ngakhale pali chipwirikitichi, Mutharika sakulankhulapo kuti tsogolo likhala lotani ndipo mmalo mwake yemwe akulankhulapo ndi nduna ya zachuma Godall Gondwe amene akukanitsitsa kuti palibe kuonjezera malipiro ponena kuti dziko lino lili pamoto malinga ndi momwe chuma chikuyendera.

Mkulu wa bungwe la Institute for Policy Interaction (IPI) Rafik Hajat akuti boma lisatenge nkhani yonyanyala ntchitoyi mwachibwana.

“Boma lionetse chidwi chifukwa ngati silisamala zingabweretse mavuto adzaoneni,” adatero Hajat polankhula ndi Tamvani Lachiwiri.

Mneneri wa chipani cha PP Ken Msonda akuti chipani chawo chakhumudwa kuti mpaka lero Mutharika sadalankhulepo kanthu, zomwe wati “nzodabwitsa”.

“Mwina poti adanena [nthawi ya kampeni] kuti adzapitiriza pamene akulu awo adalekera ndiye mwina kupitiriza kwake n’kumeneku pamene tayamba kuona masitalaka osalekeza monga zidalili nthawiwo,” adatero Msonda.

Mneneriyu adati Mutharika akuyenera auze Amalawi zomwe zichitike pamene kunyanyala ntchito kuli mkati.

Nay Billy Banda wa bungwe la Malawi Watch akuti Mutharika akuyenera kuyankhulapo pamene aliyense ali kakasi kusowa chochita.

“Mtsogoleri sayenera kulankhula wamba, n’chifukwa chake pali mneneri wake kapena nduna yokhudzidwa kuti azilankhula, koma pomene zafikapa mtsogoleriyu ayenera kulankhulapo ndithu kuti Amalawi ayembekezere zotani ndi mmene zinthu zilili,” adatero Banda.

Mkuluyu adati sakukhutira ndi momwe boma likuchitira pankhaniyi kotero akupenekera kuti kulankhula kwa Mutharika kungabweretse chiyembekezo kwa Amalawi.

“Sizikudziwika ngati sitalaka ya ogwira ntchito kumakhoti ingathe msanga, koma pamene tikudikira kuti kumabwaloko kulongosoke, ndi izi tikumvanso kuti ena ogwira ntchito m’boma ayambanso kunyanyala. Koma sitikumva kuti boma lakambirana ndi anthuwa kuti kunyanyalaku kuthe.

“Apatu ife sitikukhutira, timayembekeza kuti mwina boma lilankhulana ndi anthuwa kapena kukambirana ndi bungwe limene limamenyera ufulu wawo kuti mwina kulowerera kwawo mavutowa akhoza kutha,” adaonjeza Banda.

Koma malinga ndi mkulu wa zamalamulo kuboma Kalekeni Kaphale, bungwe la maloya la Malawi Law Society (MLS) lidakumana ndi mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika pomwe zidaoneka kuti sitalakayo ikhoza kutha posachedwa.

Boma la DPP lakhala likunena kuti mavutowa akudza kaamba ka kubedwa kwa ndalama m’boma komwe kudaonekera muulamuliro wa PP. Koma Msonda akuti iyi si nkhani.

“Ngati ndalama palibe, nanga ndalama zomwe amadzikwezera okha zija adazitenga kuti? Nanga amati azitenga kuti popeza ndalama m’bomamo akuti mulibe?” adatero Msonda.

Sabata ziwiri zapitazo zidadziwika kuti mtsogoleri wa dziko lino pamodzi ndi wachiwiri wake adzikwezera malipiro ndi K8 pa K10 iliyonse komanso nduna zake ndi sipikala wa Nyumba ya Malamulo kudzanso mtsogoleri wotsutsa. Koma Mutharika ndi wachiwiri wake Saulos Chilima adakana kuti ayambe kulandira malipirowo padakalipano kaamba ka mavuti a zachuma.

Naye mneneri wa chipani cha UDF Ken Ndanga akuti sangayankhule zambiri chifukwa sadatsatire momwe boma lakhala likuchitira pankhani yokhudza kunyanyalaku.

Komabe Ndanga wati kukambirana kukufunika kuti sitalakazi zitheretu m’dziko muno.

Koma mneneri wa Mutharika, Fredrick Ndala, komanso mneneri wa boma Kondwani Nankhumwa sadayankhe mafoni awo pamene Tamvani imati imve mbali yawo.

Nayenso mkulu wa bungwe loona za ufulu wa ogwira ntchitowa la Civil Servants Trade Union (CSTU), Servace Sakala, adakana kutsirapo ndemanga ponena kuti tilankhule ndi aboma pankhaniyi.

Related Articles

Back to top button