Nkhani

Mavuto a UDF angaphe demokalase

Listen to this article

Chipasupasu cha m’chipani chakale cholamula cha United Democratic Front (UDF) chingaopseze ulamuliro wa demokalase m’dziko muno womwe umalira kuti pakhale zipani zotsutsa zamphamvu zothandiza kuongolera pomwe chipani cholamula chikulakwitsa.

Katswiri wa phunziro la ndale kudzanso otumikiridwa pandale aikira ndemangayi potsatira mgwedegwede womwe wakula mu chipani cha UDF.

Iwo ati kufooka kwa UDF—chimodzimodzi mikangano ya m’chipani china chotsutsa chachikulu cha MCP—kupereka mwayi kwa chipani cholamula cha DPP kuyenda moyera, mosatsutsidwa pa maganizo a kayendetsedwe ka boma.

Katswiri pa maphunziro a ndale yemwenso ndi mphunzitsi pa sukulu ya ukachenjede ya Mzuzu, Noel Mbowela, wati chipani cha UDF chidali cha mphamvu polingalira kuti chidalamulapo koma awa ndi malecheleche ngati sichikonza zolakwikazi.

Iye adati ngati zipani zotsutsa zili za mphamvu, zimakakamiza chipani cholamula kuti chidzilabadira zofuna za anthu ndipo izi zimapindulira dziko.

Kuunikiraku kwadza pomwe tsopano mamulumuzana a UDF, omwe ena mwa iwo ndi a komiti yaikulu yachipanichi, agawikana ndipo kuli mbali ziwiri zomwe sizionana ndi diso labwino.

Mbali imodzi kuli Gorge nga Ntafu, mlembi wamkulu Kennedy Makwangala, Lilian Patel, Atupele Muluzi komanso aphungu onse 15 a chipanichi ku Nyumba ya Malamulo.

Mbali ina kuli Friday Jumbe yemwe adapatsidwa ulamuliro wachipani ndi wapampando wakale Bakili Muluzi, Hophmally Makande, Sam Mpasu, Humphrey Mvula komanso Ken Nsonda.

Pano mbali ya Jumbe yalengeza kuti yachotsa Makwangwala komanso Atupele pomwe ati awiriwa adalephera kukaonekera ku komiti yosungitsa mwambo yachipanichi.

Koma Msonda wati anthu asadandaule chifukwa zomwe zikuchitikazi pochotsa ena ndi njira imodzi yokonzera chipanichi.

Iye wati mavuto onse omwe ali kuchipanichi adadza ndi Bakili chifukwa chodzitengera mwa yekha zochitika m’chipanimo.

Mgwedegwede m’chipanichi udakula mwezi wa Okutobala 2011 pomwe Atupele Muluzi adabwera poyera ndikulengeza khumbo lake lodzaima nawo pa mpando wa pulezidenti m’chaka cha 2014.

Izi sizidakomere komiti yaikulu m’chipanichi yomwe idati izi ndizosemphana ndi malamulo achipanichi.

Apa chipanichi chidaitanitsa Atupele kuti akaonekere ku komiti yosungitsa mwambo yachipanichi koma iye adakana ndipo komitiyi idalengeza kuti yamuchotsa m’chipani.

Msonda wati aphungu onse akunyumba ya malamulo ali mbali ya Atupele, yemwenso ndi phungu wa dera la kumpoto cha kum’mawa kwa Machinga.

Kugwedezekaku kudakulanso pa 21 Disembala 2011 pomwe Makwangwala adatulutsa kalata yomwe Msonda wati n’kutheka idalembedwa atanamizidwa ndi Bakili Muluzi.

Kalatayo idati:

• Maudindo onse a m’chipanichi abwerera momwe adaliri pa 16 Julaye 2009 pomwe wapampando wachipanichi, Bakili Muluzi adanyamuka kupita kuchipatala ku UK ndikusiya zonse m’manja mwa mlembi wa mkulu wachipanichi.

• Ngodya zomwe zakonzedwa kuchoka pa 16 Julaye 2009 zonse zamasulidwa ndipo mamembala onse achipanichi omwe adakakamizidwa kuchoka m’chipanichi abwezeretsedwa pamaudindo awo.

• Msonkhano wa komiti yaikulu yachipani udzachitika ku likulu la chipanichi ku Limbe pa 28 Disembala 2011 nthawi ya 9 koloko m’mawa.

Apa mamulumuzana ena achipanichi komanso Msonda adati kalatayo yalembedwa mosafunsa akuluakulu achipanichi.

Iwo adati Makwangwala alibe mphamvu zoterezi chifukwa komiti yomwe ikugwira ntchito ndiyo idayenera kubweretsa poyera mfundozi ku komiti yaikulu ya chipani zisanatuluke.

Msonda wati mfundo zomwe zidalembedwa m’kalatayo, zikutanthauza kuti Bakili Muluzi ndiye adabweretsa mfundozi kuti Makwangwala alembe.

“Pa 16 pomwe akunenapo, Muluzi adatula maudindo kwa komiti yomwe ikugwira ntchito ndipo maudindowa adawatenganso atabwera kuchoka kuchipatala.

“Mu Disembala 2009, Muluzi adatulira udindo Jumbe pomwe adalengezanso kuti akusiya ndale.

“Lero wina akamati maudindo onse abwerera mwakale, akutanthauza kuti Muluzi wayambiranso ndale? Apa ife tikutsimikizirika kuti zonsezi akuchita ndi Muluzi,” adatero Msonda.

Kalatayi itangotuluka, akuluakulu achipanichi pamodzi ndi Msonda adakatenga chiletso choletsa msonkhano wa pa 28 Disembala.

Chipanichi chidaitanitsa Makwangwala komanso Atupele ku komiti yosungitsa mwambo, koma awiriwa sadatuyukire.

Apa awiriwa adachotsedwa m’chipanimo n’kusankha Hophmally Makande kuti akhale wogwirizira mpando wa mlembi wachipanichi.

Chipanichi pa 27 Disembala chidaitanitsa Bakili Muluzi kuti akaonekere ku komiti yosungitsa mwambo pa 11 Januwale 2012 koma Muluzi, pobwera kuchokera ku Zambia, adati izi nz’amkutu.

Kalata yomwe idalembedwa ndi Makande idati Muluzi akuyenera kukayankha milandu itatu.

Iyi ndiyo kusowetsa K125 miliyoni yachipanichi, kutenga katundu wachipani ndikukamulembetsa m’dzina lake komanso kuitanitsa mamembala achipanichi pamodzi ndi Makwangwala pa 21 Disembala ku zokambirana chikhalilecho alibe mphamvu zotere malinga ndi gawo 12 (b)(vi), 12(b)(vii) ndi 12(b)(ix) a malamulo achipanichi.

Mbowela wati zonsezi zikuonetsa kuti chipanichi komanso ulamuliro wa zipani zambiri ukulowera kuchiwonongeko.

Sam Banda wa m’mudzi mwa Chipoka kwa T/A Mponda m’boma la Mangochi wati chipasupasuchi chikusokoneza anthu:

“Nditsate ziti? Sitikudziwa kuti tidzavotera ndani. Akuyenera kugwirizana zochita,” adatero Banda.

Sanudi Tambula wa m’mudzi mwa Kalembo kwa T/A Kalembo m’boma la Balaka wati “chidwi ndi chipanichi chikuchoka.”

Msonda waloza chala Bakili Muluzi ndipo wakumbutsira zomwe adachita Muluzi ati potenga munthu wakunja kwa chipani—Bingu wa Mutharika—ndikumupatsa ulamuliro wa UDF pa chisankho cha 2004. Iye adati pano Muluzi wayamba kugwiritsa ntchito ena monga Makwangwala kuti azibweretsa zachilendo m’chipanichi, zomwe komiti yaikulu ikukana.

M’chaka cha 1994 pomwe chipanichi chidalowa m’boma, chipanichi chidali ndi aphungu 92 m’nyumba ya malamulo ndipo pofika 1999 n’kuti chili ndi aphungu oposa 100 chifukwa aphungu a chipani cha Alliance for Democracy (AFORD) adagwirizana ndi chipanichi.

M’chaka cha 1999 mpaka 2004 chipanichi chidali ndi aphungu 55 ndipo panthawiyi chipani cha MCP ndicho chidatenga aphungu ambiri.

Pano chipanichi chili ndi aphungu 15 okha kunyumba ya malamulo.

Related Articles

Back to top button
Translate »