Nkhani

MCP, UTM, PP ayamba kutsatsa manifesito

Kupereka makalata ofuna kudzaimira m’chisankho chikudzachi ndiye kwatha, maso tsopano ali pazomwe zipani zasanja kufuna kutukula dziko lino.

Kuunguza kwa Tamvani kwapeza kuti mfundo zomwe zipani zasanja sizikusiyana kwambiri. Zipani za UTM, MCP ndi PP atsindika nkhani ya ntchito, ulimi, maphunziro ndi magetsi.

MCP akuti yamaliza kusanja manifesito ake

Chipani cholamula cha DPP chakana kuulula manifesito ake ati chifukwa nthawi ya kampeni sidakwane. Pamene olankhulira UDF nambala zawo sizimapezeka.

Mneneri wa MCP, Maurice Munthali adati manifesito a chipani chawo atuluka koma adakana kuti tiyione ponena kuti kukhala mwambo wobweretsa poyera manifesitoyo.

Komabe iye adati manifesito yawo alongedza mfundo monga zotukula ulimi ndi kukonza misika yodalirika ya mbewu, kuthetsa vuto la magetsi, kutukula maphunziro ndi kutsitsa chiwongola dzanja pa ngongole zomwe anthu amatenga ku banki.

“Mwachitsanzo, manifesto ikuti m’miyezi 6 yoyambirira, vuto lamagetsi lidzakhala litantha. Pakutha pa chaka, banja lilironse lizidzadya katatu patsiku,” adatero Munthali.

Mneneri wa chipani cha PP Ackson Kalaile Banda adati chipanicho chasanja zodzapeleka magetsi aulere m’midzi, kuwonjezera chiwerengero cha wogwira ntchito m’boma, kukhazikitsa sabuside yopindulira aliyense komanso kuwonjezera nyengo yomwe oyendetsa magalimoto amatenga kuti akakonzeso chiphaso chawo.

“Padakali pano, ogwira ntchito m’boma alipo 25 000 koma ife takonza zoti adzafike 40 000 kuti anthu ambiri makamaka achinyamata adzapeze ntchito. Zaka zisanu zomwe munthu amatenga kuti akakonzenso chiphaso choyendetsera galimoto zimachepaa koma ife tidzawonjezera.

“M’midzimu, tidzayikamo magetsi aulere kuti anthu akumudzi moyo wawo udzasinthe ndipo sabuside tidzathetsa zosankha anthu kuti aliyense yemwe akufuna kulima azidzapeza mwayi wa sabuside,” adatero Kalaile Banda.

Mneneri wa UTM Joseph Chidanti Malunga adati manifesito yachipani idatha kale koma chipani chikadasokerera mwina pomva maganizo a anthu ena ndipo chikuyika mlingo wa nthawi yodzakwaniritsira malonjezo ake.

Mwa mfundo zina, Malunga adati chipani cha UTM chizidzawonetsetsa kuti chikulemba ntchito achinyamata 1 miliyoni pa chak.

Chidzakonza nkhani za malimidwe ndi zamaphunziro pochotsa njira yosankhira ophunzira opita ku sukulu za ukachenjede.

“Ndipo zomwe tasanja m’manifesito athu zidzachitika, mboni adzakhala Amalawi,” adatero Malunga.

Koma kadaulo pa ndale Nandin Patel wati ngakhale zipani zili ndi ufulu obenthula za m’manifesito kapena ayi, ndibwino kufulumira kuuza anthu zomwe awakonzera chifukwa zimapereka mpata kwa anthu kuti afunse momwe sakumvetsa.

“Nthawi zambiri, manifesito imangonena zomwe chipani chidzachite chikadzapambana koma poti manifesito amatuluka mochedwa, anthu sakhala ndi mpata ofunsa momwe zipanizo zidzakwaniritsire mfundozo,” adatero Patel.

Iye waunikiranso kuti manifesito abwino amayenera kufotokoza nthawi yomwe mfundo zomwe zalonjezedwazo zidzakwaniritsidwe kuti anthu azidzatha kukwenya nthawi ikakwana koma mfundo osawoneka tsogolo lake.

Mneneri wa chipani cha DPP Nicholas Dausi adati chipani chake ndichosakonzeka kudziwitsa Amalawi zomwe chidzawachitire akapatsidwanso zaka zina zisanu.

Related Articles

Back to top button