Nkhani

Mgwedegwede m’zipani wakula

Listen to this article

Mgwedegwede womwe wayanga chipani cholamula cha DPP ndi zina zotsutsa boma monga UDF ndi MCP ungabale zisankho zabwino mu 2014, waunikira katswiri pandale yemwenso ndi mphunzitsi wa zandale kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College.

 

Mkuluyu, Blessings Chinsinga, wati umu ndi mmene zimayenera kukhalira maka zisankho pulezidenti komanso a phungu zikayandikira.

Apa Chinsinga wati ichi ndichiyambi chabe ndipo pena zidzifika pa alindi mwana agwiritse, koma anthu adekhe mpaka madzi atadikha kuopa kumwa matope.

Iye wati misamuko ikuchitika m’zipani ndi imene itamangenso zipani mwatsopano, kuzisanduliza zolimba.

Sabata yatha, aphungu anayi a chipani cholamula cha DPP adauza nyuzipepala ya Weekend Nation kuti akhazikitsa gulu lomwe lidziunikira pomwe pakhota nyani mchira m’chipanichi.

Gululi lomwe woliyankhulira ndi phungu wa dera la kumwera kwa kwa mzinda kwa Blantyre, Moses Kunkuyu, lati pali aphungu 30 ndipo lidziuza mtsogoleri wa dziko lino Bingu wa Mutharika chindunji, osati phula lomwe ena omuzungulira akhala akukumata.

Ku UDF matatalazi sakutha pomwe chipanichi chagawika pawiri.

Akatakwe monga Humphrey Mvula ndi Sam Mpasu mwa ena ali pambuyo pa Friday Jumbe yemwe akugwiriziza udindo wa pulezidenti wa chipanichi kuchokera pomwe mtsogoleri wakale Bakili Muluzi adalengeza kuti wasiya ndale.

Ndipo gulu lina kuli zikanthawe monga mlembi wachipanichi, Kennedy Makwangwala, Geroge Nga Ntafu, Ibrahim Matola kudzanso aphungu 15 a chipanichi ku Nyumba ya Malamulo ali pambuyo pa mwana wa Atcheya Atupele Muluzi.

Pomwe ena akadziotche monga yemwe adali wachiwiri kwa mneneri wachipanichi, Ken Msonda, wasamuka mu UDF ndipo walowa chipani cha wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Joyce Banda cha People’s Party [PP].

Henry Phoya, yemwe adachotsedwa m’chipani cha DPP m’mbuyomu nayenso waumanga ndipo walowa MCP. Phoya adakhalapo nduna m’maboma a UDF ndi DPP.

Chinsinga wati zonsezi ndizosadabwitsa chifukwa zisankho zikayandikira andale amasinkhasinkha kolowera kuti adzachite bwino.

“Apa aliyense amayang’ana mazira omwe angamubalire kanthu akawafungatira. Pofika mu Juni zikhala zambiri zikuchitika pandale.

“Izi zikuyenera kuchitika pano chifukwa zitati zizichitika mu 2013 woponya voti angasokonekere koopsa.”

Pounikira pa andale angapo omwe akwawira kuzipani zina, iye wati kuyenda kwa anthuwa kungakhale ndi tanthauzo, mwinanso ayi.

“A Msonda adatsanzika kuti akukalera zidzukulu, koma pano akuti alowa kuchipani cha PP. Izi sizingapatse anthu chikhulupiriro mwa mkuluyu.

“Zomwe achita a Phoya zadabwitsa ambiri, ngakhale inenso. Koma izi mwina zingasinthe zingapo pandale malinga ndi momwe anthu amachionera chipani ca MCP.

“N’kutheka a Phoya abweretsa zingapo ku MCP chifukwa cha kulimba mtima kwawo komwe adaonetsa potsutsa mabilo oipa m’nyumba ya malamulo,” akutero Chinsinga.

Baziliyo Kajani wa m’mudzi mwa Chaponya kwa T/A Mzukuzuku m’boma la Mzimba wati, sakuganiza kuti mpungwepungwewu ungakonze masankho a mu 2014 kaamba koti nthawi ino ndiyoyenera kuti zipani zotsutsa zizichita ntchito yachitukuko.

“Pandale pamafunika kukhala mgwirizano n’cholinga chotukula dziko, osati zikuchitikazi zomwe sizingatipindulire.

“Zipani zotsutsa zikuyenera kupereka thandizo kuchipani cholamula, maka pankhani ya chitukuko, zomwe sizikuchitika. Izi zingadzabale ziwawa mu 2014,” adatero Kajani.

Frank Mpuno wa m’mudzi mwa Yoyola kwa T/A Masasa m’boma la Ntcheu wati masankho abwino mu 2014 angadze ngati akuluakulu a zipani akudziwitsa anthu za zomwe zikuchitikazo.

“Amatifuna panthawi ya kampeni basi. Mukadzamva kuti sitikavota osamadabwa,” akutero Mpuyo.

Mgwedegwede mu UDF udayamba m’mwezi wa Okutobala 2011 pomwe Atupele Muluzi adabwera poyera ndikulengeza kuti iye adzaima nawo pa mpando wa pulezidenti m’chaka cha 2014.

Izi sizidakomere komiti yaikulu m’chipanichi ndipo akuluakulu mmenemo adati izi n’zosemphana ndi malamulo achipani.

Apa chipanichi chidaitanitsa Atupele kuti akaonekere ku komiti yosungitsa mwambo yachipanichi koma iye adakana ndipo chidamuchotsa.

Kugwedezekaku kudabukanso pa 21 Disembala 2011 pomwe mlembi wachipanichi Kennedy Makwangwala adalemba kalata yothetsa maudindo onse.

Kulumana ku MCP kuli pakati pa mlembi wa chipanichi, Chris Daza, ndi mtsogoleri wachipani, John Tembo.

Daza wakhala akulankhula poyera kuti Tembo akuyenera kusiira utsogoleri wachipanichi m’manja mwa achinyamata, zomwe zakhala zikutsutsula Tembo.

M’mwezi wa Sepitembala chaka chatha, komiti yaikulu ya chipanichi idachotsa Daza kuti sindiyenso mlembi wachipanichi koma bwalo lamilandu lalikulu ku Lilongwe m’mwezi wa Okutobala lidabwezeretsa Daza pa mpandowo.

Pano chipanichi chalandira Phoya.

Ku DPP kwachoka aphungu angapo monga Jennifer Chilunga wa ku Zomba Nsondole yemwe adalowa chipani cha PP komanso Grace Maseko wa ku Zomba Changalume.

Related Articles

Back to top button