Nkhani

Mikangano yatha

Listen to this article

Chisangalalo chadzanso kwa Achewa a m’boma la Mwanza pomwe T/A Kanduku wa m’bomalo walengeza Lolemba pa 26 Malitchi kuti madambwe onse omwe adawatseka atsekulidwenso.

Bwanamkubwa wa boma la Mwanza, Smart Gwedemula watsimikiza zakutsekulidwa kwa madambwewo.

Kanduku adatseka madambwewo ati pokhumudwa ndi zomwe Achewa amachita poumbudza amayi pomwe akuchokera kumadzi komanso kumumenya iyeyo popanda chifukwa.

Apa Kanduku adanyanyuka ndipo adatseka madambwewo chaka chatha.

Mafumu a Chichewa adauza Tamvani kuti zomwe akunena Kanduku kuti nyau zidamuumbudza ndi bodza koma kuti iye amakakamiza mafumu a Chichewo kuti alowe Chingoni popeza iye ndiwachingoni.

Mafumu angapo adaonetsa Tamvani mithini, mnyoni, zibonga ndi zishango zomwe mafumu Achichewawa amagwiritsa ntchito ati mokakamizidwa ndi Kanduku.

Mwezi wangothawu nduna ya maboma ang’ono, Henry Mussa idaitanitsa Kanduku.

Related Articles

Back to top button