Chichewa

Mkazi wansanje achekacheka mnzake

Listen to this article

 

Bwalo la milandu la majisitireti ku Mchinji masiku apitawa lidalamula kuti mayi wansanje amene adachekacheka mayi mnzake ndi mpeni pakhosi ndi kunkhope akagwire jere la miyezi 12 koma lidamumasula ponena kuti asadzapezekenso ndi mlandu wina kwa chaka chimodzi ndi theka.

Woimira boma pamilandu, Thom Waya, adauza bwalolo kuti mkazi wansanjeyo, Chimwemwe Fanizo, wa zaka 21, adafuna kuvulaza mwana wa mkazi mnzake wa miyezi 7 ndi mpeni ati popeza mwamuna wake ankapereka thandizo kwa mwanayo.

Wasiya kuonetsa mabala ake m’chipatala
Wasiya kuonetsa mabala ake m’chipatala

Waya adati mpeniwo udasempha mwanayo yemwe adali kumsana ndi kulunjika pakhosi la mayi ake. Mbereko yomwe adaberekera mwanayo idamasuka moti adagwa pansi ndipo achisoni adamutola ndi kuthawa naye.

Izi sizidakondweretse Fanizo, yemwe adalikumba liwiro kuthamangitsa munthu amene adathawitsa mwanayo, mpeni uli m’manja. Komatu apa nkuti mkaziyo atamuchekacheka mnzakeyo malo anayi. Anthu adamugwira ndipo adapita naye kupolisi pamodzi ndi wovulazidwayo.

Izi zidachitika mmawa wa pa 6 January pa Mkanda Trading Centre.

Apolisi adamutsekulira mlandu wovulaza munthu, womwe womangidwayo adauvomera pamaso pa woweruza, majisitireti Rodwell Meja.

Malinga ndi Waya, bwalolo silidachedwe kugamula mlanduwo chifukwa woimbidwa mlandu sadatayitse khotilo nthawi povomera kulakwa.

Podandaulira bwalolo kuti limuganizire popereka chilango, Fanizo adati adapalamula mlanduwo chifukwa adachita kuputidwa ndi wodandaulayo, Tsala Wasiya, pokhala pachibwenzi ndi mwamuna wake.

Pogamula mlanduwo, Meja adati bwalo lake lidamupeza ndi mlandu wovulaza ndipo ayenera kulangidwa molingana ndi malamulo a dziko lino, koma adapereka chilango chosakhwimacho poganizira kuti adachita kuputidwa komanso poti sadatayitse bwalolo nthawi povomereza kulakwa kwake.

Meja adapereka chilango choti Fanizo akaseweze chaka chimodzi kundende koma adati kundendeko sapitako bola asapezekenso ndi mlandu kwa miyezi 18. Adamulola kuti azipita kwawo, mlandu watha. Adatinso ngati sakukhutira chi chigamulocho ali ndi ufulu kuchita apilo.

Msangulutso udacheza ndi Wasiya, yemwe ali ndi zaka 20, kuti umve mbali yake ndi mmene zidakhalira kuti zifike mpakana kuvulazidwa chonchi.

Iye adati adalidi paubwenzi ndi Daniel Nkhomo ndipo ubwenziwu utafumbira adapezeka ndi pakati.

Iye adati ngakhale awiriwa sadalowane, Nkhomo adali kupereka chisamaliro chonse chomwe munthu oyembekezera amafuna mpaka mwana adabadwa.

“Koma ndidadabwa kuti pomwe mwana wanga adakwanitsa sabata zitatu, abambowa adakatenga mkazi wina kwa Msundwe ndipo adasiya kupereka chithandizo,” iye adatero.

Wasiya adati koma patadutsa miyezi iwiri bamboyu adayambiranso kuthandiza mwana wakeyu ndipo awiriwa amatchayirana lamya mwanayu akadwala zomwe sizimamkomera mkazi mnzakeyo.

“Tsiku lina ndidatumiza uthenga palamya kuti andiimbire kaamba koti mwana adali atadwala matenda otsekula m’mimba. Mkazi wakeyu ndiye adandiimbira ndi kunditukwana,” Wasiya adatero.

Iye adati mphuno salota sadadziwe kuti Fanizo adali ndi mangawa ndipo adakagula mpeni ndi kukanoletsa kumatchini ndi cholinga chofuna kuthana naye.

Wasiya adati patsikuli adali akuchokera kumsika ndipo Fanizo adamutchingira kutsogolo.

“Adandifunsa kuti bwanji ndimaimba lamya ya mwamuna wake? Bwanji adandisiya ine nkutenga iyeyo ngati ndili naye mwana wake? Nkudzati ndipanga za iwe, pompo mpeni sololu kuti abaye mwana kumsana. Mpeniwu udafikira pakhosi panga,” adalongosola Wasiya

Iye adati koma adali wodabwa kuti ngakhale adavulazidwa chomwechi Fanizo ndi mfulu ndipo adampititsa kwawo.

Msangulutso udachezanso ndi Wasiya Titus, bambo wa mayi wovulazidwayu.

Iye adati sakudziwa kuti mlanduwu uli pati kaamba koti atafufuza kupolisi ya Mchinji adauzidwa kuti Fanizo adamasulidwa ndi abwalo la milandu.

“Abwalo la milandu sadamve mbali ya mwana wanga yemwe sakupezabe bwino, kodi adamtulutsa bwanji ife okhudzidwa kulibe? Komabe ndipita konko kuti ndikamve umo zidayendera,” adatero Titus.

Pakalipano Wasiya wanenetsa kuti zivute motani akufuna mwamunayu amukwatire basi.

“Ine ndikufuna mwamunayu andikwatire chifukwa wandipatsitsa mabala, moti amuna ena sadzandisiriranso ayi. Ndipo mkazi wakeyu achita bwanji nsanje ndi ine, popeza ine ndiye ndidali woyamba ndipo ndimafunika kuchita nsanjezo ndineyo osati iyeyo wachiwiri ayi,” adalankhula motsindika Wasiya.

Pomwe Msangulutso udacheza ndi mwamunayo Lachinayi lapitali palamya, iye adati Wasiya adali mkazi wachibwenzi pomwe Fanizo adali wapanyumba.

“Banja langa latha ndi Fanizo ndipo ndidamtumiza kwawo. Pakadalipano ndikupanga dongosolo loti ndikwatire Wasiya, si nanga ndamuonongetsa,” adatero Nkhomo.n

Related Articles

Back to top button
Translate »