Chichewa

Mpira uthera panjira wosewera atamwalira

Listen to this article

 

Anthu akugwedeza mitu yopanda nyanga ku Choma, m’boma la Mzimba kaamba ka imfa ya mnyamata wa Fomu 3 pasukulu ya sekondale ya Choma yemwe adaombana ndi goloboyi poti agwire mpira ali paliwiro lamtondo wadooka lokagoletsa Lachisanu lapitalo.

Patsikulo, timu yomwe Isaac Phiri wa zaka 20 amasewera imapimana mphamvu ndi timu yachisodzera ya pa sukulupo.

football

Isaac amasewera ngati wogoletsa.

Malinga ndi mphunzitsi wamkulu pasukulupa, Mathews Phiri, yemwenso amaonerera masewerowa, izi zidachitika patangodutsa mphindi 30 mpira utayamba ndipo udathera pomwepo.

Phiri adati Isaac yemwe adali wogoletsa wodalilika, adanyamuka ndi mpira mwa liwiro zedi ndi cholinga chokagoletsa, ndipo atayandikira golo kuti aponyere muukonde naye goli adachoka pagolo ndi kuombana ndi mnyamatayo.

Iye adati, apa onse adagwa pansi ndipo Isaac adayamba kudzigwiragwira moonetsa kuti ali muululu woopsa.

Malinga ndi lipoti la chipatala, kuombana pachifuwa kwa awiriwo kudachititsa avulazane mkati komanso womwalirayo apweteke kapamba.

“Tidathamangira konko, pamodzi ndi achipatala omwe adalinso pompo, tidayesa kumutsira madzi koma sizidathandize ndipo apa mpamene tidathamangira naye kuchipatala chomwe chilli pafupi ndi bwalo lamaseweroli komwe atamupima adatiuza kuti watisiya,” Phiri adatero.

Iye adati masewerawo, omwe amakonzekera masewero akulu ndi timu ya sukulu ya pulaiveti ya Chiume adathera pomwepo ndipo aliyense sakumvetsa zomwe zidachitikazo.

Koma Levi Mwale yemwe ndi dokotala wa timu ya dziko lino adati ngozi zotere sizichitikachitika.

Mwale adati nthawi zambiri zikachitika zimakhala kuti wosewera mpira wameza lilime lomwe limatseka modutsa mpweya.

Iye adati vuto ndi loti masewera ambiri m’dziko muno, amaseweredwa opanda akatswiri a za udotolo.

“Anthu sadziwa kuti munthu akavulala akusewera mpira, amasamalidwa bwanji,” Mwale adatero.

Iye adati ndi zachisoni kuti imfa zoterozi zimagwa chifukwa chosowa chidziwitso.

“Tikufunika tiphunzitsidwe kasamalidwe ka ovulala mu mpira, kuyambira matimu a supa ligi, maligi aang’ono komanso a m’madera ndi m’sukulu,” Mwale adatero.

Polankhulapo mneneri wa apolisi m’chigawo cha kumpoto Maurice Chapola adati Issac yemwe amachokera m’mudzi mwa Msafiri T/A Mtwalo m’bomalo adamwalira kaamba kovulalira mkati. Iye adati adavumbulutsa izi ndi a chipatala cha Mzuzu.

Chapola adatsimikiza kuti Isaac adakomoka ataombana ndi goli ndipo achipatala cha Choma ndiwo adalengeza za imfa yake ndi kutumiza thupi lake ku chipatala cha Mzuzu kukafufuza chidadzetsa imfayi.

Related Articles

Back to top button