Friday, August 19, 2022
  • About Us
  • ImagiNATION
  • Rate Card
  • Contact Us
The Nation Online
Advertisement
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Columns
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation
No Result
View All Result
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Columns
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation
No Result
View All Result
No Result
View All Result
Home Chichewa Nkhani

Msika wa osewera watentha

by Bobby Kabango
21/08/2015
in Nkhani
2 min read
0
Share on FacebookShare on TwitterShare on WhatsAppShare on LinkedinLinkedinShare via Email

Pamene matimu ali kopumira kukonzekera ndime yachiwiri ya 2015 TNM Super League, msika wa osewera wafika potentha pamene matimu ali kalikiriki kugula ndi kugulitsa osewera n’cholinga chofuna kuchita bwino m’ligiyi ikayamba m’ndime yachiwiri.

Tiyamba ndi timu yomwe ikuteteza ligiyi yomwenso ikutsogola ndi mapointi 32. Iyi ndi Big Bullets, yomwe padakalipano ikukambirana ndi timu ya Mzuni FC kuti itenge mnyamata womwetsa zigoli wa ku Burundi, Aimable Niyikiza, amene tikukamba pano ali kukampu ya Bullets.bullets

Timuyi ikufunanso itenge mnyamata wosewera pakati kutimu ya Azam, Yamikani Chester, koma timu yakeyi ikukaniza kuti wosewerayu sali pamalonda.

Bullets yatenganso Chisomo Mpachika wosewera kumbuyo m’timu ya Dedza Young Soccer ngakhale timu yake ikukaniza kumugulitsa ponena kuti ngati Bullets ikumufuna ndiye iwapatse Sankhani Mkandawire ndi Yamikani Fodya.

Tipite ku Silver Strikers yomwe yakanika kutenga goloboyi wa Mighty Be Forward Wanderers Richard Chipuwa ndipo mmalo mwake yatenga Bester Phiri, yemwenso amagwirira pagolo ku Wanderers.

Padakalipano Wanderers yatchaja Silver kuti ipereke K2 miliyoni pokana kuti Silver itenge wosewerayu pangongole.

Silver yatenga kale John Banda yemwe adali pangongole ku Young Soccer kuchokera ku Evirom pamtengo wa K500 000. Timuyi ikufunanso kutenga mnyamata wosewera kumanzere chakumbuyo kwa Epac, Dalitso Mwase, pamtengo wa K2 miliyoni.

Nayo Wanderers ikufuna kutenga Boston Kabango kuchokera ku Epac pamtengo wa K3 miliyoni. Koma Silver ndi Fisd Wizards nawonso maso awo ali pa mnyamata yemweyu.

Wanderers ndi Bullets akulimbirananso Chester, yemwe Azam ikukanitsitsa kugulitsa. Wanderers yaonetsanso chidwi kufuna kutenga Kelvin Hara, Dave Mwalughali, George Hawadi ndi Hastings Banda komanso George Kasambara kuchokera kutimu ya Chilumba Barracks ngakhale timuyi ikukana kuti sakuwagulitsa osewera awo.

Timuyi ikufunanso itenge John Lanjesi wa Civo pamtengo wa K4.5 miliyoni.

Azam Tigers yatenga kale Abraham Kamwendo kuchokera ku Blantyre United ndipo yatoleranso osewera ena achisodzera pamene Moyale yatenga Komani Msiska yemwe akutsogola ndi zigoli ku Chilumba.

Red Lions yagula wosewera wapakati wa Zomba United Stanley Dube.

Mphunzitsi wa timuyi Collins Nkuna akuti wakhala akuyendayenda m’midzimu ndipo wapeza osewera ambiri m’boma la Salima.

Civo United sikumveka kuti ikusaka osewera mitunda iti koma timuyi yaitanitsa Josophat Kwalira kuchokera ku Dedza Young Soccer.

Wizards yatola Godfrey Masonda. Fisd ikufunanso kugula Precious Msosa kuchokera ku Wanderers.

Msikawu utsekedwa pa 18 September usiku ligiyi isanayambirenso pa 19 September.

Previous Post

Samalani: Kwabuka matenda a chimanga

Next Post

Sickness grounds Poly student at home

Related Posts

Patrick sakubwerera mmbuyo pa chikopa
Nkhani

Patrick Mwaungulu ndi katakwe pokankha chikopa

July 24, 2022
Chilima: Change the mindset toward development
Nkhani

A Chilima abwera poyera

July 1, 2022
Nkhani

Achilima awachepetsera mphamvu zaulamuliro

June 24, 2022
Next Post

Sickness grounds Poly student at home

Opinions and Columns

Business Unpacked

Why public debt should worry every patriotic Malawian

August 18, 2022
Rise and Shine

How to triumph in interviews

August 18, 2022
My Turn

Making briquettes at Malasha

August 15, 2022
Candid Talk

When parents demand more

August 14, 2022

Malawi-Music.com Top10

Trending Stories

  • Court snubs tenants on govt houses

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • ‘Blantyre derby could have fetched more’

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Why graft cases stall

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • World Bank protests K14bn ICT contract

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Govt appoints university working committee

    0 shares
    Share 0 Tweet 0

  • Values
  • Our Philosophy
  • Editorial policy
  • Advertising Policy
  • Code of Conduct
  • Plagiarism disclaimer
  • Disclaimer
  • Privacy Policy
  • Terms of use

© 2022 Nation Publications Limited. All Rights Reserved.

No Result
View All Result
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Columns
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation

© 2020 Nation Publications Limited. All Rights Reserved.

This website uses cookies. By continuing to use this website you are giving consent to cookies being used. Visit our Privacy and Cookie Policy.