Nkhani

Mswati akhale chitsanzo kwa achinyamata

Listen to this article

Pulezidenti Joyce Banda wati mfumu yachingoni yomwe angoidzoza kumene, Mswati Kanjedza Gomani yachisanu ikhale chitsanzo kwa achinyamata.

Banda amalankhula izi Lamulungu pa 5 Ogasiti pomwe adali mlendo wolemekezeka ku mwabowo ku Lizulu m’boma la Ntcheu.

Mwazina Banda adapempha anthu andale kuti asasokoneze mfumuyi, yomwe ndi ya zaka 17.

“Tithandize mfumu yathu kuti igwire bwino ntchito. Fumu ikhale yachilungamo, yodziwa kuweruza milandu; amati milandu sagula ndi chipanda cha mowa.

“Komanso, ngati boma, ndife osangalala kukhala ndi mfumu yachinyamata ngati imeneyi chifukwa ikhala chitsanzo chabwino kwa achinyamata.

‘Zomwe izichita mfumuyi achinyamata adzitengera iyo,” adatero Banda.

Mswati Gomani walowa ufumuwo kutsatira imfa ya bambo ake, Willard Kanjedza Gomani yachinayi yomwe idamwalira mwezi wa Sepitembala mu 2009.

Pamwambowo, kudabwera akuluakulu andale komanso amabungwe.

Nayo mfumu yaikulu ya angoni m’dziko la Mozambique, T/A Zimtambira, idali nawo pamwambowo.

Related Articles

Back to top button