Chichewa

Muli mphamvu mu ukhondo

Bungwe la Water for People Malawi (WPM) lomwe cholinga chake n’kuonetsetsa kuti anthu m’dziko muno azimwa madzi aukhondo, komanso kukhala ndi zimbudzi zabwino lati mu ukhondo muli mphamvu chifukwa munthu sadwaladwala choncho amagwira ntchito molimbika.

Bungweli layankhula izi Lachiwiri ku Chiradzulu pa mwambo wosayinirana ndondoneko za ntchito za ukhondo ndi khonsolo ya m’bomalo.

Chavula: Ukhondo umathandiza kupewa matenda

Malingana ndi mkulu wa bungweli m’dziko muno Kate Harawa, ndondomekoyi ndi ya zaka zitatu ndipo bungweli laika padera K2.5 biliyoni yogwirira ntchitoyi m’bomalo.

“Tikufuna anthu onse, zipatala komanso sukulu zonse za m’bomali zikhale ndi madzi ndi zimbudzi zaukhondo kuti mavuto omwe amadza kaamba kosowa zipangizozi achepe,” iye adatero.

Kuonjezera apo, mkuluyu adati anthu aziphunzitsidwa ukhondo wa pa thupi ndi pakhomo pawo.

Iye adafotokoza kuti boma la Chirazulu lidatsankhidwa mwa maboma 7 omwe bungweli lidachitamo kafukufuku  chifukwa cha chidwi chomwe lidaonetsa poyankha mwa msanga mafunso komanso kukula kwa vuto la kusowekera kwa zipangizo zaukhondo.

Bwanankubwa wa khonsoloyi Reinghard Kaweta Chavula adati mwa anthu 100 aliwonse a m’bomali, 73 ndi omwe amakwanitsa kupeza madzi abwino ndipo 63 okha ndi omwe ali ndi zipangizo za ukhondo monga zimbudzi.

“Kubwera kwa ndondomekoyi kwapereka chiyembekezo ndipo tili ndi chikhulupiriro kuti  pakutha pa zaka zitatu boma la Chirazulu lidzakhala limodzi mwa maboma omwe akuchita bwino kwambiri pankhani ya ukhondo,” iye adatero.

Chavula adati izi zidzathandiza kupewa matenda monga wotsegula m’mimba omwe amadza kaamba ka kusowekera kwa madzi abwino ndi  ukhondo.

Iye adati pamapeto pake anthu azidzakhala kalikiliki ndi ntchito zotukula maanja awo.

Related Articles

Back to top button