Nkhani

Musandinjate, ndinali ku ndende komweko

A Jonathan Ng’ambi Lachinayi sabata yatha adaseketsa omvera milandu m’khoti la Chitipa atapempha woweruza milandu kuti asawapititse ku ndende ati chifukwa adali atangotuluka kumene ku ndende komwe adali koseweza chifukwa chopalamula mlandu winanso.

Chimene chidatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke mnyanga nchakuti, patsikulo a Ng’ambi, omwe ndi a zaka 22, adakaonekera m’khoti kukayankha milandu iwiri: wothyola nyumba ya a Simon Mtambo komanso woba nyemba zodzadza tini za ndalama zokwana K39 000 m’mudzi wa Masyesye m’dera la mfumu Mwabulambya m’bomalo.

Malingana ndi woimira boma pa milandu mayi Lucy Phiri, a Ng’ambi adapalamula milanduyi pa 16 June chaka chomwe chino pamene mwini nyumba adali kulima pa munda wina omwe uli kuseri kwa nyumba yake.

A Phiri adauza bwalolo: “Pa tsikulo, mwini nyumba adali kulima munda wake kuseli kwa nyumba ndipo adaona a Ng’ambi akutuluka m’nyumba yawo ndi tini ya nyemba. Apa mpamene a Mtambo adafuula kuti anthu akufuna kwabwino awathandize ndipo nthawi pang’ono, khwimbi la anthu lidafika pa malopo n’kugwira a Ng’ambi omwe adawatengera ku polisi.”

Ndipo pa tsiku loonekera m’khoti, a Ng’ambi adavomera milandu yonse iwiri koma adadabwitsa anthu pamene adapempha khotilo kuti lipereke chilango chofewa ponena kuti iwo adali atangotuluka kumene ku ndende komwe adakasewezanso jele atapalamula milandu yofanana ndi yomweyi.

“Ndikupempha bwalo la milandu kuti lindipatse chilango chofewa. Munthune ndatuluka posachedwapa ku ndende kotero ndidakali kudyerera ufulu umenewu, ku ndende ndi kumanda,” adapempha motero a Ng’ambi.

Komabe, m’kupempha kwawo, a Phiri adauza bwalolo kuti a Ng’ambi ngoyenera chilango chokhwima kwambiri ponena kuti iwo ndi kabwerebwere wodziwika bwino, wokonda kupalamula milandu ikuluikulu imenenso imapereka chiopsezo komanso mantha kwa anthu amene amafuna kuchita chitukuko chosiyasiyana.

“A Ng’ambi ndi munthu wosokoneza kwambiri. Si munthu wofunika kukhala ndi anthu. Mkuluyu akufunika azikhala ku ndende chifukwa akuopseza anthu amene ali ndi chidwi chotukula dziko. Kotero kuti ndikupempha bwaloli kuti lipereke chilango chokhwima kuti ena atengerepo phunziro,” adatero a Phiri.

Ndipo popereka chigamulo, woweruza milandu a Billy Ngosi adagwirizana ndi woimira boma pa milandu wa polisiyo ponena kuti mchitidwe woberana pophwanya nyumba ukuchulukira m’bomalo omwe ndi woopsa kwambiri.

“Zikuoneka kuti a Ng’ambi ndi munthu wosamva ndipo ndi munthu woopsa ndipo safuna kukhala ndi anthu ndi chifukwa chake atapita ku ndende ulendo woyamba sadaphunzirepo kanthu ndi kusintha khalidwe lawo lonunkha.

“Chifukwa cha ichi, ndikuwalamula kuti akakhale ku ndende miyezi 72 pa mlandu wothyola nyumba komanso miyezi ina 18 pa mlandu wa kuba komwe akaseweze ndipo zilango zonsezi ziyendera limodzi,” adalamula motero a Ngosi.

A Ng’ambi amachokera m’mudzi mwa Nthambalika m’dera la Mfumu Mwabulambya m’bomalo.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button