Mutharika apempha bata

Peter Mutharika, yemwe adapambana pa chisankho cha pa 21 May, dzulo adapempha Amalawi kuti apite patsogolo ndi kukhala wogwirizana ndi a mtendere potukula dziko lino.

Polankhula dzulo ku Kamuzu Stadium mumzinda wa Blantyre pamwambo wolandira ulemerero wa dziko lino kuchokera kwa asilikali, Mutharika adati Amalawi ayenera kuyanjana potukula dziko lino.

Mutharika kuonetsa lupanga la ulemerero pamwambowo

“Tonse tiyenera kudekha ndi kuthana ndi umphawi. Amalawi alankhula ndipo zofuna zawo zikwaniritsidwe. Icho chitiluzanitsa chiposa icho chitisemphanitsa. Ndine mtsogoleri wa Amalawi onse, kaya adandivotera kaya sanandivotere,” adatero Mutharika pamwambo umene padafika khwimbi la anthu.

Iye adapempha a mipingo ngakhalenso ogwira ntchito m’boma kuti apewe kulowerera pandale.

Ndipo polankhulapo za zipolowe zimene zidadza ndi otsatira chipani cha MCP ena amene adakwiya ndi kusankhidwa kwa Mutharika, mtsogoleri wa dziko linoyo adapempha otsatira chipani chake cha DPP kuti asabwenzere.

“N’zachisoni kuti amayi ena otsatira DPP amenyedwa ndi kuvulidwa koma palibe mabungwe a za amayi amene alankhulapo kanthu chifukwa amayiwo ndi a DPP. Chonde osabwenzera choipa,” adatero Mutharika.

Pamwambowo, padafika nduna yaikulu ya dziko la Tanzania, Kassim Majaliwa, komanso nduna zoimirira maiko a Zambia, Zimbabwe ndi Mozambique  komanso oimira bungwe la mgwirizano wa maiko la African Union.

Mtsogoleri wakale wa dziko lino Bakili Muluzi, yemwe adali nawo pamwambowo komanso pomwe Mutharika amamulumbiritsa Lachiwiri, adati Amalawi ayenera kuyanjana.

“Ndikuwafunira zabwino a Mutharika. Tonse tiyenera kusangalala komanso kugwirizana potukula dziko lathu,” adatero Muluzi.

Mutharika  ndi womutsatira Everton Chimulirenji adapeza ma voti oposa 1.9 miliyoni pomwe omutsatira wake, Lazarus Chakwera wa MCP ndi womutsatrira wake Sidik Mia adapeza mavoti 1.7 miliyoni.

Iyi ndi ndime yachiwiri komanso yomaliza ya Mutharika kulamulira dziko lino.

Share This Post